< 1 Chroniques 18 >

1 Il advint, après cela, que David battit les Philistins et qu'il les mit en fuite; et il leur enleva Geth avec ses bourgs.
Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo.
2 Il vainquit Moab, et les fils de Moab lui furent asservis; et ils lui payèrent un tribut.
Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.
3 David vainquit aussi, dans le pays d'Hémath, Adraazar, roi de Suba, qui s'était mis en campagne pour se rendre maître des rives de l'Euphrate.
Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
4 Et David prit aux vaincus mille chars, sept mille chevaux et vingt mille piétons; puis, il énerva les attelages de tous les chars, et n'en garda que cent.
Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
5 Et le Syrien de Damas marcha au secours d'Adraazar, roi de Suba, et David tua au Syrien vingt-deux mille hommes.
Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000.
6 Et David mit une garnison dans la Syrie de Damas, et les Syriens lui furent asservis; ils lui payèrent un tribut. Et le Seigneur protégea David partout où il porta ses armes.
Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.
7 Et David prit les colliers d'or que portaient les serviteurs d'Adraazar, et il les consacra dans Jérusalem.
Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu.
8 Et David recueillit à Mathabeth (Métébac), et dans les principales villes d'Adraazar, une prodigieuse quantité d'airain, dont Salomon se servit pour fabriquer la mer d'airain, et les colonnes et tous les vases d'airain.
Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.
9 Cependant Thoa (Thu), roi d'Hémath, apprit que David avait taillé en pièces toute l'armée d'Adraazar.
Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba,
10 Et il envoya vers David son fils Aduram (Jedduram), pour lui demander la paix et le bénir à cause de sa victoire sur Adraazar; car Thoa était ennemi d'Adraazar. Et tous les vases d'or, d'argent et d'airain,
anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.
11 Le roi David les consacra au Seigneur de même que l'argent et l'or qu'il avait pris à toutes les nations: à l'Idumée, à Moab, aux fils d'Ammon, aux Philistins et aux fils d'Amalec.
Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.
12 Et Abessa, fils de Sarvia, tailla en pièces quatre-vingt mille Philistins dans le val d'Aïlon.
Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.
13 Et il mit dans la vallée une garnison, et tous les Iduméens furent asservis à David, et le Seigneur protégea David partout où il porta ses armes.
Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
14 Ainsi, David régna sur tout Israël, et il jugea tout son peuple selon l'équité.
Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse.
15 Joab, fils de Sarvia, commandait l'armée; Josaphat, fils d'Achilud, recueillait les actes publics.
Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika;
16 Sadoc, fils d'Achitob, et Achimélech, fils d'Abiathar, étaient prêtres, et Susa (Sasa), scribe.
Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi;
17 Et Banaïas, fils de Joad, commandait Chéléthi et Phéléthi, et les fils de David étaient les premiers lieutenants du roi.
Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.

< 1 Chroniques 18 >