< Masalimo 132 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Inu Yehova, kumbukirani Davide ndi mavuto onse anapirira.
שיר המעלות זכור-יהוה לדוד-- את כל-ענותו
2 Iye analumbira kwa Yehova ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
אשר נשבע ליהוה נדר לאביר יעקב
3 “Sindidzalowa mʼnyumba mwanga kapena kugona pa bedi langa:
אם-אבא באהל ביתי אם-אעלה על-ערש יצועי
4 sindidzalola kuti maso anga agone, kapena zikope zanga ziwodzere,
אם אתן שנת לעיני לעפעפי תנומה
5 mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
עד-אמצא מקום ליהוה משכנות לאביר יעקב
6 Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
הנה-שמענוה באפרתה מצאנוה בשדי-יער
7 “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo; tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
נבואה למשכנותיו נשתחוה להדם רגליו
8 ‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira, Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
קומה יהוה למנוחתך אתה וארון עזך
9 Ansembe anu avekedwe chilungamo; anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’”
כהניך ילבשו-צדק וחסידיך ירננו
10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu, musakane wodzozedwa wanu.
בעבור דוד עבדך-- אל-תשב פני משיחך
11 Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;
נשבע-יהוה לדוד אמת-- לא-ישוב ממנה מפרי בטנך-- אשית לכסא-לך
12 ngati ana ako azisunga pangano langa ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa, pamenepo ana awo adzakhala pa mpando wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
אם-ישמרו בניך בריתי-- ועדתי זו אלמדם גם-בניהם עדי-עד-- ישבו לכסא-לך
13 Pakuti Yehova wasankha Ziyoni, Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
כי-בחר יהוה בציון אוה למושב לו
14 “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi; ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
זאת-מנוחתי עדי-עד פה-אשב כי אותיה
15 Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri; anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
צידה ברך אברך אביוניה אשביע לחם
16 Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso, ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
וכהניה אלביש ישע וחסידיה רנן ירננו
17 “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
שם אצמיח קרן לדוד ערכתי נר למשיחי
18 Ndidzaveka adani ake manyazi, koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
אויביו אלביש בשת ועליו יציץ נזרו

< Masalimo 132 >