< Masalimo 135 >

1 Tamandani Yehova. Tamandani dzina la Yehova; mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
הללו-יה הללו את-שם יהוה הללו עבדי יהוה
2 amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
שעמדים בבית יהוה-- בחצרות בית אלהינו
3 Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino; imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
הללו-יה כי-טוב יהוה זמרו לשמו כי נעים
4 Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake, Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
כי-יעקב בחר לו יה ישראל לסגלתו
5 Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
כי אני ידעתי כי-גדול יהוה ואדנינו מכל-אלהים
6 Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
כל אשר-חפץ יהוה עשה בשמים ובארץ-- בימים וכל-תהמות
7 Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
מעלה נשאים מקצה הארץ ברקים למטר עשה מוצא-רוח מאוצרותיו
8 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
שהכה בכורי מצרים-- מאדם עד-בהמה
9 Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto, kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
שלח אותת ומפתים--בתוככי מצרים בפרעה ובכל-עבדיו
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu ndi kupha mafumu amphamvu:
שהכה גוים רבים והרג מלכים עצומים
11 Sihoni mfumu ya Aamori, Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a ku Kanaani;
לסיחון מלך האמרי ולעוג מלך הבשן ולכל ממלכות כנען
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa, cholowa cha anthu ake Aisraeli.
ונתן ארצם נחלה-- נחלה לישראל עמו
13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
יהוה שמך לעולם יהוה זכרך לדר-ודר
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa, ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
כי-ידין יהוה עמו ועל-עבדיו יתנחם
15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
עצבי הגוים כסף וזהב מעשה ידי אדם
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya;
פה-להם ולא ידברו עינים להם ולא יראו
17 makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
אזנים להם ולא יאזינו אף אין-יש-רוח בפיהם
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
כמוהם יהיו עשיהם-- כל אשר-בטח בהם
19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova; inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
בית ישראל ברכו את-יהוה בית אהרן ברכו את-יהוה
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova; Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
בית הלוי ברכו את-יהוה יראי יהוה ברכו את-יהוה
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova.
ברוך יהוה מציון-- שכן ירושלם הללו-יה

< Masalimo 135 >