< Levitiko 1 >

1 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati,
The Lord called Moses and spoke to him from the Tent of Meeting, saying,
2 “Aliyense wa inu ngati abwera ndi nsembe kwa Yehova kuchokera pa ziweto zake, choperekacho chikhale ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.
“Go and speak to the Israelites and tell them: When you present an offering to the Lord, you may bring as your offering an animal from the herd of cattle or the flock of sheep or goats.
3 “‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire.
If your offering is a burnt offering from a herd of cattle, you must offer a male without any defects. Bring it to the entrance of the Tent of Meeting so it can be accepted before the Lord.
4 Munthuyo asanjike dzanja lake pa mutu pa nsembe yopserezayo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake.
Put your hand on the head of the burnt offering, so it can be accepted on your behalf to make you right.
5 Pambuyo pake aphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo ansembe, ana a Aaroni, atenge magazi ake ndi kuwawaza mbali zonse za guwa lansembe limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.
You are to kill the bull in the Lord's presence, and Aaron's sons, the priests, are to take the blood and sprinkle it on all sides of the altar at the entrance to the Tent of Meeting.
6 Munthuyo asende nsembe yopserezayo ndi kuyidula nthulinthuli.
Then you are to skin the burnt offering and cut it into pieces.
7 Ndipo ana a Aaroni, wansembe uja asonkhe moto pa guwa ndi kuyalapo nkhuni pa motopo.
The sons of Aaron the priest shall start a fire on the altar and put wood on it.
8 Kenaka ana a Aaroni, wansembe uja, ayike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe pa nkhuni zimene zili paguwapo.
Then the priests shall carefully place the pieces, including the head and the fat, on the wood burning on the altar.
9 Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.
You shall wash the insides and legs with water, and the priest shall burn all of it on the altar as a burnt offering, a food offering, to be accepted by the Lord.
10 “‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema.
If your offering is a burnt offering from a flock, either sheep or goats, you must offer a male without any defects.
11 Ayiphere kumpoto kwa guwa, pamaso pa Yehova, ndipo ana a Aaroni amene ndi ansembe, awaze magazi ake mbali zonse za guwalo.
You are to kill it on the north side of the altar in the Lord's presence, and Aaron's sons, the priests, are to take the blood and sprinkle it on all sides of the altar.
12 Kenaka ayidule nyamayo nthulinthuli, ndipo wansembe ayike nthulizo pa guwa, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo ayike zonsezi pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa.
Then you are to cut it into pieces, and the priest shall carefully place the pieces, including the head and the fat, on the wood burning on the altar.
13 Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe abwere nazo zonse ndi kuzitentha pa guwa. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chotentha pa moto, fungo lokomera Yehova.
You shall wash the insides and legs with water, and the priest shall burn all of it on the altar as a burnt offering, a food offering, to be accepted by the Lord.
14 “‘Koma ngati chopereka kwa Yehova ndi nsembe yopsereza ya mbalame, ndiye ikhale njiwa kapena mawunda.
If your offering to the Lord is a burnt offering of birds, you are to offer a turtledove or a young pigeon.
15 Wansembe abwere nayo ku guwa, ayidule mutu moyipotola ndi kutentha mutuwo pa guwa. Magazi ake awathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa.
The priest shall take it to the altar, twist off its head, and burn it on the altar. Its blood shall be drained out on the side of the altar.
16 Iye achotse chithokomiro pamodzi ndi nthenga zake zomwe ndi kuzitaya ku malo wotayirako phulusa, kummawa kwa guwalo.
He must remove the crop and the feathers, and throw them to the east side of the altar into the ash pile.
17 Kenaka ayingʼambe pakati, koma asachotse mapiko. Ndipo wansembe ayiwotche pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, yowotcha pa moto ndiponso ya fungo lokomera Yehova.
He shall tear it open by its wings, but not completely apart. The priest is to burn it on the altar on the burning wood. It is a burnt offering, a food offering, to be accepted by the Lord.

< Levitiko 1 >