< Mika 7 >

1 Hankàñe amako! fa manahake i nipòk’ amo vokan’ asara fa natontoñeoy, tsy am-pirotorotom-baloboke ho haneñe; ndra valoham-boa hampilelalela ty fiaiko.
Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
2 Fa nifaoheñ’ an-tane atoy t’indaty mañori-Kake, tsy ao ty mahity am’ondatio; songa miampitse handrendreke lio, sindre mifañoroñe an-karato o mpirahalahio.
Anthu opembedza atha mʼdziko; palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala. Anthu onse akubisalirana kuti aphane; aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.
3 Fità-roe ty mahatafetetse o sata rati’eo; ipaia’ i roandriañey naho takea’ i mpizakay ty vokàñe; aboa’ ty bey ty fikitrohan-tro’e, vaho rarè’ iereo hitraoke.
Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita.
4 Hoe hìsatse ty soa am’iereo, hoe vovom-patike ty mahity ama’e; i andro ampitsatohe’o mpijilojiloy: tondroke ty fitilihañe azo; ho doboñe iereo henane zay.
Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga, munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga. Tsiku limene alonda ako ananena lafika, tsiku limene Mulungu akukuchezera. Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.
5 Ko miato rañetse, ko mirampy aman-atehena; amy màndre añ’araña’o eoy, itaò o soñi’oo.
Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.
6 Fa mañamavo an-drae’e ty ana-dahy, miatreatre an-drene ty anak’ ampela, ty vinanto-ampela aman-drafoza’e ampela; rafelahi’ondatio t’indaty añ’akiba’e ao.
Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake, mwana wamkazi akuwukira amayi ake, mtengwa akukangana ndi apongozi ake, adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.
7 Aa naho izaho, hitamà Iehovà; ho liñisako i Andrianañaharem-pandrombahakoy; hijanjiñe ahy t’i Andrianañahareko.
Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo, ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga adzamvetsera.
8 Ko mirebeke ahy, ry mpalaiñ’ ahio, ndra t’ie mikorovoke, mbe hitroatse; ndra mitobok’ añ’ieñe ao, Iehovà ro hazavàko.
Iwe mdani wanga, usandiseke! Ngakhale ndagwa, ndidzauka. Ngakhale ndikukhala mu mdima, Yehova ndiye kuwunika kwanga.
9 Ho vavèko ty haviñera’ Iehovà amy t’ie nandilatse ama’e, ampara’ te ihalalia’e ho ahy, naho ampijadoña’e zakam-pañisohañe; ie hakare’e mb’an-kazavàm-b’eo, vaho ho treako ty havantaña’e.
Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndinamuchimwira, mpaka ataweruza mlandu wanga ndi kukhazikitsa chilungamo changa. Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika; ndidzaona chilungamo chake.
10 Ho oni’ i rafelahikoy izay, vaho ho saroña’ ty hasalarañe ty nanao amako ty hoe: Aia t’Iehovà Andrianañahare’o? Ho sambae’ o masokoo, ie ho lialiàñe hoe fotak’ an-dalañe eo henane zay.
Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi nadzagwidwa ndi manyazi, iye amene anandifunsa kuti, “Ali kuti Yehova Mulungu wako?” Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga; ngakhale tsopano adzaponderezedwa ngati matope mʼmisewu.
11 Ho androm-pampitroarañe o kijoli’oo amy andro zay, hibolea’ i Hake mb’eo mbe’o.
Idzafika nthawi yomanganso makoma anu, nthawi yokulitsanso malire anu.
12 Ho androm-pitotsahañ’ ama’o, boak’ Asore naho i Mitsraime, boake Mitsraime pak’amy sakay; eka, boak’an-driake pak’an-driake, vaho boak’am-bohitse pak’am-bohitse,
Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto, ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
13 Le ho koake i taney ty amo mpimone’eo, ho vale’ ty hatsivokaram-pitoloña’ iareo.
Dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.
14 Araho an-kobai’o ondati’oo, i lia-rain-dova’o rerek’ añ’ala ao, an-teñateñan-tane marorok’ aoy; andrazo mb’e Basane naho mb’e Gilade mb’eo iereo manahake tañ’andro haehae.
Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale.
15 Manahake tañ’andro nañakarako azo an-tane Mitsraime ao, le hampiboahako raha fanjaka.
“Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga, ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
16 Ho oni’ o kilakila’ ondatio le ho salatse ndra te maozatse; hamihim-palie am-pitàñe vaho ho valagìñe an-dravembia.
Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzagwira pakamwa pawo ndipo makutu awo adzagontha.
17 Ie hitsela deboke hoe mereñe, hititititike t’ie miakatse an-kijoly ao hoe merembitike hirik’ an-tane ao; hangebahebake t’ie miheo mb’am’ Iehovà Andrianañaharentika, vaho hañeveñe ama’o iereo.
Adzabwira fumbi ngati njoka, ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi. Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo; mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu ndipo adzachita nanu mantha.
18 Ia t’i Andrianañahare hañirinkiriñe Azo, Mpañafa-kakeo, naho mampipoke ty fiolà’ o honkahonkan-dova’eo! Tsy tana’e nainai’e ty haviñera’e, vaho ifalea’e ty fiferenaiñañe.
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
19 Hiferenaiña’e indraike tika, ho lialiàm-pandia’e o hakeon-tikañeo; Eka! hahifi’o an-driake lalek’ ao o tahi’ iareoo.
Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
20 Ho tolora’o havantañañe t’Iakobe, naho fiferenaiñañe t’i Avrahame, i nifantà’o aman-droae’ay haehae izay.
Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.

< Mika 7 >