< 역대하 14 >

1 아비야가 그 열조와 함께 자매 다윗성에 장사되고 그 아들 아사가 대신하여 왕이 되니 그 시대에 그 땅이 십년을 평안하니라
Tsono Abiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Asa mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake ndipo pa masiku ake, dziko linakhala pa mtendere kwa zaka khumi.
2 아사가 그 하나님 여호와 보시기에 선과 정의를 행하여
Asa anachita zabwino ndi zolungama pamaso pa Yehova Mulungu wake.
3 이방 제단과 산당을 없이하고 주상을 훼파하며 아세라 상을 찍고
Iye anachotsa maguwa achilendo ndi malo opembedzerapo mafano, anaphwanya zipilala za miyala yachipembedzo ndi kugwetsa mafano a Asera.
4 유다 사람을 명하여 그 열조의 하나님 여호와를 구하게 하며 그 율법과 명령을 행하게 하고
Asa analamula Yuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kumvera malamulo ndi zolamulira zake.
5 또 유다 모든 성읍에서 산당과 태양상을 없이하매 나라가 그 앞에서 평안함을 얻으니라
Iye anachotsa malo opembedzera mafano ndi maguwa ofukizira lubani mu mzinda uliwonse wa mu Yuda, ndipo mu ufumu wake munali mtendere pa nthawi ya ulamuliro wake.
6 여호와께서 아사에게 평안을 주셨으므로 그 땅이 평안하여 여러해 싸움이 없은지라 저가 견고한 성읍들을 유다에 건축하니라
Asa anamanga mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda pakuti dziko linali pa mtendere. Panalibe amene anachita naye nkhondo mʼzaka zimenezo, pakuti Yehova anamupatsa mpumulo.
7 아사가 일찌기 유다사람에게 이르되 우리가 우리 하나님 여호와를 찾았으므로 이 땅이 아직 우리 앞에 있나니 우리가 이 성읍들을 건축하고 그 주위에 성곽과 망대와 문과 빗장을 만들자 우리가 주를 찾았으므로 주께서 우리에게 사방의 평안을 주셨느니라 하고 이에 저희가 성읍을 형통하게 건축하였더라
Iye anati kwa Yuda “Tiyeni timange mizinda iyi ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi zotchinga. Dzikoli likanali lathu chifukwa tafuna Yehova Mulungu wathu; tinamufuna Iye ndipo watipatsa mpumulo mbali zonse.” Kotero iwo anamanga ndi kukhala pa ulemerero.
8 아사의 군대는 유다 중에서 큰 방패와 창을 잡는 자가 삼십만이요 베냐민 중에서 작은 방패를 잡으며 활을 당기는 자가 이십 팔만이라 다 큰 용사더라
Asa anali ndi ankhondo 300,000 ochokera ku Yuda, okhala ndi zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndiponso ankhondo 280,000 ochokera ku Benjamini, okhala ndi zishango ndi mauta. Onsewa anali ankhondo amphamvu ndi olimba mtima.
9 구스 사람 세라가 저희를 치려하여 군사 백만과 병거 삼백승을 거느리고 마레사에 이르매
Zera wa ku Kusi anapita kukamenyana nawo ali ndi gulu lalikulu kwambiri la asilikali ndi magaleta 300 ndipo anafika mpaka ku Maresa.
10 아사가 마주 나아가서 마레사의 스바다 골짜기에 진치고
Asa anapita kukakumana naye ndipo anakhala pa mizere yawo ya nkhondo mʼchigwa cha Zefata pafupi ndi Maresa.
11 그 하나님 여호와께 부르짖어 가로되 여호와여 강한 자와 약한자 사이에는 주밖에 도와줄 이가 없사오니 우리 하나님 여호와여, 우리를 도우소서 우리가 주를 의지하오며 주의 이름을 의탁하옵고 이 많은 무리를 치러왔나이다 여호와여, 주는 우리 하나님이시오니 원컨대 사람으로 주를 이기지 못하게 하옵소서 하였더니
Kenaka Asa anafuwulira Yehova Mulungu wake ndipo anati “Yehova palibe wina wofanana nanu kuti angathandize anthu opanda mphamvu pakati pa amphamvu. Tithandizeni Inu Yehova Mulungu wathu pakuti ife timadalira Inu ndipo mʼdzina lanu ife tabwera kudzalimbana ndi gulu la ankhondo lalikulu kwambiri ngati ili. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu, musalole kuti munthu akupambaneni.”
12 여호와께서 구스 사람을 아사와 유다 사람 앞에서 쳐서 패하게 하시니 구스 사람이 도망하는지라
Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Ayuda. Akusi anathawa,
13 아사와 그 좇는자가 구스 사람을 쫓아 그랄까지 이르매 이에 구스 사람이 엎드러지고 살아 남은 자가 없었으니 이는 여호와 앞에서와 그 군대 앞에서 패망하였음이라 노략한 물건이 심히 많았더라
ndipo Asa ndi ankhondo ake anawathamangitsa mpaka ku Gerari. Gulu lonse lalikulu lija la Akusi linaphedwa. Sanapezeke mmodzi wamoyo pakati pawo. Iwo anakanthidwa pamaso pa Yehova ndi asilikali ake. Anthu a ku Yuda anatenga katundu wambiri olanda ku nkhondo.
14 여호와께서 그랄 사면 모든 성읍 백성을 두렵게 하시니 무리가 그 모든 성읍을 치고 그 가운데 있는 많은 물건을 노략하고
Iwo anawononga midzi yonse yozungulira Gerari pakuti mantha aakulu wochokera kwa Yehova anagwera anthuwo. Analanda katundu wa midzi yonse, popeza kunali katundu wambiri kumeneko.
15 또 짐승 지키는 천막을 치고 양과 약대를 많이 이끌고 예루살렘으로 돌아왔더라
Anakathiranso nkhondo misasa ya anthu oweta ziweto ndipo anatenga nkhosa zambiri, mbuzi ndi ngamira. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

< 역대하 14 >