< תהילים 68 >
למנצח לדוד מזמור שיר יקום אלהים יפוצו אויביו וינוסו משנאיו מפניו׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane; adani ake athawe pamaso pake.
כהנדף עשן תנדף כהמס דונג מפני אש יאבדו רשעים מפני אלהים׃ | 2 |
Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali. Monga phula limasungunukira pa moto, oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
וצדיקים ישמחו יעלצו לפני אלהים וישישו בשמחה׃ | 3 |
Koma olungama asangalale ndi kukondwera pamaso pa Mulungu; iwo akondwere ndi kusangalala.
שירו לאלהים זמרו שמו סלו לרכב בערבות ביה שמו ועלזו לפניו׃ | 4 |
Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando, mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo; dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
אבי יתומים ודין אלמנות אלהים במעון קדשו׃ | 5 |
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
אלהים מושיב יחידים ביתה מוציא אסירים בכושרות אך סוררים שכנו צחיחה׃ | 6 |
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
אלהים בצאתך לפני עמך בצעדך בישימון סלה׃ | 7 |
Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu, pamene munayenda kudutsa chipululu,
ארץ רעשה אף שמים נטפו מפני אלהים זה סיני מפני אלהים אלהי ישראל׃ | 8 |
dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula, pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai. Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
גשם נדבות תניף אלהים נחלתך ונלאה אתה כוננתה׃ | 9 |
Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu; munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
חיתך ישבו בה תכין בטובתך לעני אלהים׃ | 10 |
Anthu anu anakhala mʼmenemo ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
אדני יתן אמר המבשרות צבא רב׃ | 11 |
Ambuye analengeza mawu, ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
מלכי צבאות ידדון ידדון ונות בית תחלק שלל׃ | 12 |
“Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro; mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
אם תשכבון בין שפתים כנפי יונה נחפה בכסף ואברותיה בירקרק חרוץ׃ | 13 |
Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto, mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva, nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
בפרש שדי מלכים בה תשלג בצלמון׃ | 14 |
Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko, zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.
הר אלהים הר בשן הר גבננים הר בשן׃ | 15 |
Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero; mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
למה תרצדון הרים גבננים ההר חמד אלהים לשבתו אף יהוה ישכן לנצח׃ | 16 |
Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri, pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira, kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
רכב אלהים רבתים אלפי שנאן אדני בם סיני בקדש׃ | 17 |
Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
עלית למרום שבית שבי לקחת מתנות באדם ואף סוררים לשכן יה אלהים׃ | 18 |
Pamene Inu munakwera mmwamba, munatsogolera a mʼndende ambiri; munalandira mphatso kuchokera kwa anthu, ngakhale kuchokera kwa owukira, kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.
ברוך אדני יום יום יעמס לנו האל ישועתנו סלה׃ | 19 |
Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
האל לנו אל למושעות וליהוה אדני למות תוצאות׃ | 20 |
Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa; Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
אך אלהים ימחץ ראש איביו קדקד שער מתהלך באשמיו׃ | 21 |
Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake, zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
אמר אדני מבשן אשיב אשיב ממצלות ים׃ | 22 |
Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani; ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
למען תמחץ רגלך בדם לשון כלביך מאיבים מנהו׃ | 23 |
Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu, pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”
ראו הליכותיך אלהים הליכות אלי מלכי בקדש׃ | 24 |
Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu; mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
קדמו שרים אחר נגנים בתוך עלמות תופפות׃ | 25 |
Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo; pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
במקהלות ברכו אלהים יהוה ממקור ישראל׃ | 26 |
Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu; tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
שם בנימן צעיר רדם שרי יהודה רגמתם שרי זבלון שרי נפתלי׃ | 27 |
Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera, pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda, ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
צוה אלהיך עזך עוזה אלהים זו פעלת לנו׃ | 28 |
Kungani mphamvu zanu Mulungu; tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
מהיכלך על ירושלם לך יובילו מלכים שי׃ | 29 |
Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu, mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
גער חית קנה עדת אבירים בעגלי עמים מתרפס ברצי כסף בזר עמים קרבות יחפצו׃ | 30 |
Dzudzulani chirombo pakati pa mabango, gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu. Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva. Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
יאתיו חשמנים מני מצרים כוש תריץ ידיו לאלהים׃ | 31 |
Nthumwi zidzachokera ku Igupto; Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
ממלכות הארץ שירו לאלהים זמרו אדני סלה׃ | 32 |
Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi imbirani Ambuye matamando. (Sela)
לרכב בשמי שמי קדם הן יתן בקולו קול עז׃ | 33 |
Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba amene amabangula ndi mawu amphamvu.
תנו עז לאלהים על ישראל גאותו ועזו בשחקים׃ | 34 |
Lengezani za mphamvu za Mulungu, amene ulemerero wake uli pa Israeli amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
נורא אלהים ממקדשיך אל ישראל הוא נתן עז ותעצמות לעם ברוך אלהים׃ | 35 |
Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika; Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake. Matamando akhale kwa Mulungu!