< תהילים 59 >
למנצח אל תשחת לדוד מכתם בשלח שאול וישמרו את הבית להמיתו הצילני מאיבי אלהי ממתקוממי תשגבני׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Pamene Sauli anatumiza anthu kuti akalondere nyumba ya Davide ndi cholinga choti amuphe. Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu; munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.
הצילני מפעלי און ומאנשי דמים הושיעני׃ | 2 |
Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.
כי הנה ארבו לנפשי יגורו עלי עזים לא פשעי ולא חטאתי יהוה׃ | 3 |
Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.
בלי עון ירוצון ויכוננו עורה לקראתי וראה׃ | 4 |
Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!
ואתה יהוה אלהים צבאות אלהי ישראל הקיצה לפקד כל הגוים אל תחן כל בגדי און סלה׃ | 5 |
Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.
ישובו לערב יהמו ככלב ויסובבו עיר׃ | 6 |
Iwo amabweranso madzulo akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyendayenda mu mzinda.
הנה יביעון בפיהם חרבות בשפתותיהם כי מי שמע׃ | 7 |
Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo; iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo, ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”
ואתה יהוה תשחק למו תלעג לכל גוים׃ | 8 |
Koma Inu Yehova, mumawaseka, mumayinyoza mitundu yonseyo.
עזו אליך אשמרה כי אלהים משגבי׃ | 9 |
Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa.
אלהי חסדו יקדמני אלהים יראני בשררי׃ | 10 |
Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.
אל תהרגם פן ישכחו עמי הניעמו בחילך והורידמו מגננו אדני׃ | 11 |
Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu, kuopa kuti anthu anga angayiwale. Mwa mphamvu zanu, lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.
חטאת פימו דבר שפתימו וילכדו בגאונם ומאלה ומכחש יספרו׃ | 12 |
Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo chifukwa cha mawu a milomo yawo, iwo akodwe mʼkunyada kwawo. Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula
כלה בחמה כלה ואינמו וידעו כי אלהים משל ביעקב לאפסי הארץ סלה׃ | 13 |
muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo.
וישובו לערב יהמו ככלב ויסובבו עיר׃ | 14 |
Iwo amabweranso madzulo, akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyenda mu mzinda.
המה ינועון לאכל אם לא ישבעו וילינו׃ | 15 |
Iwo amayendayenda kufuna chakudya ndipo amawuwa ngati sanakhute.
ואני אשיר עזך וארנן לבקר חסדך כי היית משגב לי ומנוס ביום צר לי׃ | 16 |
Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu, mmawa ndidzayimba zachikondi chanu; pakuti ndinu linga langa, pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.
עזי אליך אזמרה כי אלהים משגבי אלהי חסדי׃ | 17 |
Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.