< תהילים 66 >

למנצח שיר מזמור הריעו לאלהים כל-הארץ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo. Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
זמרו כבוד-שמו שימו כבוד תהלתו 2
Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
אמרו לאלהים מה-נורא מעשיך ברב עזך יכחשו לך איביך 3
Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
כל-הארץ ישתחוו לך--ויזמרו-לך יזמרו שמך סלה 4
Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” (Sela)
לכו וראו מפעלות אלהים נורא עלילה על-בני אדם 5
Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
הפך ים ליבשה--בנהר יעברו ברגל שם נשמחה-בו 6
Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
משל בגבורתו עולם-- עיניו בגוים תצפינה הסוררים אל-ירימו (ירומו) למו סלה 7
Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.
ברכו עמים אלהינו והשמיעו קול תהלתו 8
Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
השם נפשנו בחיים ולא-נתן למוט רגלנו 9
Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
כי-בחנתנו אלהים צרפתנו כצרף-כסף 10
Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.
הבאתנו במצודה שמת מועקה במתנינו 11
Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
הרכבת אנוש לראשנו באנו-באש ובמים ותוציאנו לרויה 12
Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
אבוא ביתך בעולות אשלם לך נדרי 13
Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
אשר-פצו שפתי ודבר-פי בצר-לי 14
Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
עלות מיחים אעלה-לך עם-קטרת אילים אעשה בקר עם-עתודים סלה 15
Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. (Sela)
לכו-שמעו ואספרה כל-יראי אלהים אשר עשה לנפשי 16
Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
אליו פי-קראתי ורומם תחת לשוני 17
Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga.
און אם-ראיתי בלבי-- לא ישמע אדני 18
Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera;
אכן שמע אלהים הקשיב בקול תפלתי 19
koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
ברוך אלהים-- אשר לא-הסיר תפלתי וחסדו מאתי 20
Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

< תהילים 66 >