< מִשְׁלֵי 1 >
משלי שלמה בן-דוד-- מלך ישראל | 1 |
Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
לדעת חכמה ומוסר להבין אמרי בינה | 2 |
Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo; kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
לקחת מוסר השכל צדק ומשפט ומשרים | 3 |
kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru, akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
לתת לפתאים ערמה לנער דעת ומזמה | 4 |
Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera, achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
ישמע חכם ויוסף לקח ונבון תחבלות יקנה | 5 |
Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
להבין משל ומליצה דברי חכמים וחידתם | 6 |
kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
יראת יהוה ראשית דעת חכמה ומוסר אוילים בזו | 7 |
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
שמע בני מוסר אביך ואל-תטש תורת אמך | 8 |
Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
כי לוית חן הם לראשך וענקים לגרגרתך | 9 |
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
בני-- אם-יפתוך חטאים אל-תבא | 10 |
Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere.
אם-יאמרו לכה אתנו נארבה לדם נצפנה לנקי חנם | 11 |
Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;
נבלעם כשאול חיים ותמימים כיורדי בור (Sheol ) | 12 |
tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje. (Sheol )
כל-הון יקר נמצא נמלא בתינו שלל | 13 |
Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
גורלך תפיל בתוכנו כיס אחד יהיה לכלנו | 14 |
Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
בני--אל-תלך בדרך אתם מנע רגלך מנתיבתם | 15 |
Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
כי רגליהם לרע ירוצו וימהרו לשפך-דם | 16 |
Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.
כי-חנם מזרה הרשת-- בעיני כל-בעל כנף | 17 |
Nʼkopanda phindu kutchera msampha mbalame zikuona!
והם לדמם יארבו יצפנו לנפשתם | 18 |
Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe; amangodzitchera okha msampha!
כן--ארחות כל-בצע בצע את-נפש בעליו יקח | 19 |
Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.
חכמות בחוץ תרנה ברחבות תתן קולה | 20 |
Nzeru ikufuwula mu msewu, ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
בראש המיות תקרא בפתחי שערים בעיר--אמריה תאמר | 21 |
ikufuwula pa mphambano ya misewu, ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
עד-מתי פתים-- תאהבו-פתי ולצים--לצון חמדו להם וכסילים ישנאו-דעת | 22 |
“Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
תשובו לתוכחתי הנה אביעה לכם רוחי אודיעה דברי אתכם | 23 |
Tamverani mawu anga a chidzudzulo. Ine ndikukuwuzani maganizo anga ndi kukudziwitsani mawu anga.
יען קראתי ותמאנו נטיתי ידי ואין מקשיב | 24 |
Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
ותפרעו כל-עצתי ותוכחתי לא אביתם | 25 |
Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale.
גם-אני באידכם אשחק אלעג בבא פחדכם | 26 |
Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
בבא כשאוה (כשואה) פחדכם-- ואידכם כסופה יאתה בבא עליכם צרה וצוקה | 27 |
Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
אז יקראנני ולא אענה ישחרנני ולא ימצאנני | 28 |
“Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
תחת כי-שנאו דעת ויראת יהוה לא בחרו | 29 |
Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
לא-אבו לעצתי נאצו כל-תוכחתי | 30 |
popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
ויאכלו מפרי דרכם וממעצתיהם ישבעו | 31 |
Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
כי משובת פתים תהרגם ושלות כסילים תאבדם | 32 |
Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
ושמע לי ישכן-בטח ושאנן מפחד רעה | 33 |
Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”