< תהילים 6 >

למנצח בנגינות על-השמינית מזמור לדוד ב יהוה אל-באפך תוכיחני ואל-בחמתך תיסרני 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide. Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.
חנני יהוה כי אמלל-אני רפאני יהוה--כי נבהלו עצמי 2
Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
ונפשי נבהלה מאד ואת (ואתה) יהוה עד-מתי 3
Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
שובה יהוה חלצה נפשי הושיעני למען חסדך 4
Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
כי אין במות זכרך בשאול מי יודה-לך (Sheol h7585) 5
Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda? (Sheol h7585)
יגעתי באנחתי--אשחה בכל-לילה מטתי בדמעתי ערשי אמסה 6
Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
עששה מכעס עיני עתקה בכל-צוררי 7
Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
סורו ממני כל-פעלי און כי-שמע יהוה קול בכיי 8
Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
שמע יהוה תחנתי יהוה תפלתי יקח 9
Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.
יבשו ויבהלו מאד--כל-איבי ישבו יבשו רגע 10
Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

< תהילים 6 >