< תהילים 57 >

למנצח אל-תשחת לדוד מכתם-- בברחו מפני-שאול במערה ב חנני אלהים חנני-- כי בך חסיה נפשי ובצל-כנפיך אחסה-- עד יעבר הוות 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo, pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo. Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu mpaka chiwonongeko chitapita.
אקרא לאלהים עליון לאל גמר עלי 2
Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba, kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
ישלח משמים ויושיעני-- חרף שאפי סלה ישלח אלהים חסדו ואמתו 3
Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.
נפשי בתוך לבאם-- אשכבה להטים בני-אדם--שניהם חנית וחצים ולשונם חרב חדה 4
Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.
רומה על-השמים אלהים על כל-הארץ כבודך 5
Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba; mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
רשת הכינו לפעמי-- כפף נפשי כרו לפני שיחה נפלו בתוכה סלה 6
Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.
נכון לבי אלהים נכון לבי אשירה ואזמרה 7
Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu mtima wanga ndi wokhazikika. Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
עורה כבודי--עורה הנבל וכנור אעירה שחר 8
Dzuka moyo wanga! Dzukani zeze ndi pangwe! Ndidzadzuka mʼbandakucha.
אודך בעמים אדני אזמרך בלאמים 9
Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
כי-גדל עד-שמים חסדך ועד-שחקים אמתך 10
Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba; kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.
רומה על-שמים אלהים על כל-הארץ כבודך 11
Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba, mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

< תהילים 57 >