< תהילים 56 >
למנצח על-יונת אלם רחקים-- לדוד מכתם באחז אותו פלשתים בגת ב חנני אלהים כי-שאפני אנוש כל-היום לחם ילחצני | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati. Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo.
שאפו שוררי כל-היום כי-רבים לחמים לי מרום | 2 |
Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada.
יום אירא-- אני אליך אבטח | 3 |
Ndikachita mantha ndimadalira Inu.
באלהים אהלל דברו באלהים בטחתי לא אירא מה-יעשה בשר לי | 4 |
Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
כל-היום דברי יעצבו עלי כל-מחשבתם לרע | 5 |
Tsiku lonse amatembenuza mawu anga; nthawi zonse amakonza zondivulaza.
יגורו יצפינו (יצפונו)--המה עקבי ישמרו כאשר קוו נפשי | 6 |
Iwo amakambirana, amandibisalira, amayangʼanitsitsa mayendedwe anga ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.
על-און פלט-למו באף עמים הורד אלהים | 7 |
Musalole konse kuti athawe; mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
נדי ספרתה-אתה שימה דמעתי בנאדך הלא בספרתך | 8 |
Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
אז ישובו אויבי אחור ביום אקרא זה-ידעתי כי-אלהים לי | 9 |
Adani anga adzabwerera mʼmbuyo pamene ndidzalirira kwa Inu. Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
באלהים אהלל דבר ביהוה אהלל דבר | 10 |
Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda, mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
באלהים בטחתי לא אירא מה-יעשה אדם לי | 11 |
mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
עלי אלהים נדריך אשלם תודת לך | 12 |
Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu; ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
כי הצלת נפשי ממות-- הלא רגלי מדחי להתהלך לפני אלהים-- באור החיים | 13 |
Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa ndi mapazi anga kuti ndingagwe, kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kwa moyo.