< מִשְׁלֵי 26 >

כשלג בקיץ--וכמטר בקציר כן לא-נאוה לכסיל כבוד 1
Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola, ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.
כצפור לנוד כדרור לעוף-- כן קללת חנם לא (לו) תבא 2
Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira, ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.
שוט לסוס מתג לחמור ושבט לגו כסילים 3
Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu, choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.
אל-תען כסיל כאולתו פן-תשוה-לו גם-אתה 4
Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.
ענה כסיל כאולתו פן-יהיה חכם בעיניו 5
Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.
מקצה רגלים חמס שתה-- שלח דברים ביד-כסיל 6
Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.
דליו שקים מפסח ומשל בפי כסילים 7
Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
כצרור אבן במרגמה-- כן-נותן לכסיל כבוד 8
Kupereka ulemu kwa chitsiru zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.
חוח עלה ביד-שכור ומשל בפי כסילים 9
Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
רב מחולל-כל ושכר כסיל ושכר עברים 10
Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda, ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.
ככלב שב על-קאו-- כסיל שונה באולתו 11
Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.
ראית--איש חכם בעיניו תקוה לכסיל ממנו 12
Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.
אמר עצל שחל בדרך ארי בין הרחבות 13
Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango, mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”
הדלת תסוב על-צירה ועצל על-מטתו 14
Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake, momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.
טמן עצל ידו בצלחת נלאה להשיבה אל-פיו 15
Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale; zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.
חכם עצל בעיניו-- משבעה משיבי טעם 16
Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.
מחזיק באזני-כלב-- עבר מתעבר על-ריב לא-לו 17
Munthu wongolowera mikangano imene si yake ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.
כמתלהלה הירה זקים-- חצים ומות 18
Monga munthu wamisala amene akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
כן-איש רמה את-רעהו ואמר הלא-משחק אני 19
ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake, amene amati, “Ndimangoseka chabe!”
באפס עצים תכבה-אש ובאין נרגן ישתק מדון 20
Pakasowa nkhuni, moto umazima; chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.
פחם לגחלים ועצים לאש ואיש מדונים (מדינים) לחרחר-ריב 21
Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto, ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.
דברי נרגן כמתלהמים והם ירדו חדרי-בטן 22
Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma; chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.
כסף סיגים מצפה על-חרש-- שפתים דלקים ולב-רע 23
Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
בשפתו ינכר שונא ובקרבו ישית מרמה 24
Munthu wachidani amayankhula zabwino pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
כי-יחנן קולו אל-תאמן-בו כי שבע תועבות בלבו 25
Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire, pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
תכסה שנאה במשאון תגלה רעתו בקהל 26
Ngakhale amabisa chidani mochenjera, koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.
כרה-שחת בה יפול וגולל אבן אליו תשוב 27
Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha; ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.
לשון-שקר ישנא דכיו ופה חלק יעשה מדחה 28
Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka, ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.

< מִשְׁלֵי 26 >