< תהילים 1 >

אשרי האיש-- אשר לא הלך בעצת רשעים ובדרך חטאים לא עמד ובמושב לצים לא ישב 1
Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
כי אם בתורת יהוה חפצו ובתורתו יהגה יומם ולילה 2
Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
והיה-- כעץ שתול על-פלגי-מים אשר פריו יתן בעתו--ועלהו לא-יבול וכל אשר-יעשה יצליח 3
Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
לא-כן הרשעים כי אם-כמץ אשר-תדפנו רוח 4
Sizitero ndi anthu oyipa! Iwo ali ngati mungu umene umawuluzidwa ndi mphepo.
על-כן לא-יקמו רשעים--במשפט וחטאים בעדת צדיקים 5
Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo, kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.
כי-יודע יהוה דרך צדיקים ודרך רשעים תאבד 6
Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.

< תהילים 1 >