< איוב 39 >

הידעת--עת לדת יעלי-סלע חלל אילות תשמר 1
“Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera? Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
תספר ירחים תמלאנה וידעת עת לדתנה 2
Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere? Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
תכרענה ילדיהן תפלחנה חבליהם תשלחנה 3
Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo; pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
יחלמו בניהם ירבו בבר יצאו ולא-שבו למו 4
Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo; kenaka amachoka ndipo sabwereranso.
מי-שלח פרא חפשי ומסרות ערוד מי פתח 5
“Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani amamasula zingwe zake?
אשר-שמתי ערבה ביתו ומשכנותיו מלחה 6
Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake, nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
ישחק להמון קריה תשאות נגש לא ישמע 7
Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda; ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
יתור הרים מרעהו ואחר כל-ירוק ידרוש 8
Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.
היאבה רים עבדך אם-ילין על-אבוסך 9
“Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone mu gome lako usiku?
התקשר-רים בתלם עבתו אם-ישדד עמקים אחריך 10
Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
התבטח-בו כי-רב כחו ותעזב אליו יגיעך 11
Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake? Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
התאמין בו כי-ישוב (ישיב) זרעך וגרנך יאסף 12
Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako ndi kumuyika ku malo opunthira?
כנף-רננים נעלסה אם-אברה חסידה ונצה 13
“Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira, koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.
כי-תעזב לארץ בציה ועל-עפר תחמם 14
Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi ndipo amafundidwa ndi nthaka,
ותשכח כי-רגל תזורה וחית השדה תדושה 15
nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa, ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.
הקשיח בניה ללא-לה לריק יגיעה בלי-פחד 16
Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake; Imayiwala zoti inavutika powabala.
כי-השה אלוה חכמה ולא-חלק לה בבינה 17
Chifukwa Mulungu anayimana nzeru, simvetsa kanthu kalikonse.
כעת במרום תמריא תשחק לסוס ולרכבו 18
Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga, imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
התתן לסוס גבורה התלביש צוארו רעמה 19
“Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?
התרעישנו כארבה הוד נחרו אימה 20
Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira, ukali wake nʼkumachititsa mantha?
יחפרו בעמק וישיש בכח יצא לקראת-נשק 21
Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
ישחק לפחד ולא יחת ולא-ישוב מפני-חרב 22
Iye sachita mantha, saopa chilichonse; sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.
עליו תרנה אשפה להב חנית וכידון 23
Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.
ברעש ורגז יגמא-ארץ ולא-יאמין כי-קול שופר 24
Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha; satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.
בדי שפר יאמר האח-- ומרחוק יריח מלחמה רעם שרים ותרועה 25
Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali, kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.
המבינתך יאבר-נץ יפרש כנפו לתימן 26
“Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako, ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?
אם-על-פיך יגביה נשר וכי ירים קנו 27
Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?
סלע ישכן ויתלנן-- על שן-סלע ומצודה 28
Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku; chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.
משם חפר-אכל למרחוק עיניו יביטו 29
Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye; maso ake amachionera patali chinthucho.
ואפרחו יעלעו-דם ובאשר חללים שם הוא 30
Ana ake amayamwa magazi, ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”

< איוב 39 >