< Jérémie 3 >

1 Dis-leur: "S’Il arrive qu’un homme répudie sa femme, et que celle-ci, après l’avoir quitté, devienne l’épouse d’un autre, se peut-il qu’il la reprenne de nouveau? Un tel pays n’en serait-il pas tout à fait déshonoré? Or, toi, tu t’es prostituée à de nombreux amants et tu reviendrais à moi! dit l’Eternel.
“Ngati munthu asudzula mkazi wake ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo? Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri? Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri. Komabe bwerera kwa ine,” akutero Yehova.
2 Lève les yeux vers les collines et regarde: où ne t’es-tu pas abandonnée? Pour eux, tu te postais sur les routes comme fait le Bédouin dans le désert, et ainsi tu as souillé le pays par tes débauches et ton inconduite.
“Tayangʼana ku zitunda zowuma. Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama? Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako, ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu. Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu ndi ntchito zanu zoyipa.
3 Dussent les ondées bienfaisantes te manquer, les pluies tardives faire défaut, tu avais le front d’une courtisane, tu refusais de rougir!
Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula, ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe. Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere; ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
4 Sans doute, à l’heure présente, tu t’écries en t’adressant à moi: "O mon père, tu es le guide de ma jeunesse;
Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
5 me gardera-t-il éternellement rancune? Conservera-t-il toujours son ressentiment?" Voilà comme tu parles, et tu commets les pires fautes, et triomphes dans le mal!"
kodi mudzandikwiyira nthawi zonse? Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’ Umu ndimo mmene umayankhulira, koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”
6 L’Eternel me dit au temps du roi Josias: "As-tu vu ce que faisait Israël, la nation renégate? Elle allait sur toute montagne élevée, sous tout bois verdoyant, et s’y livrait à la prostitution.
Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko.
7 Je me disais: Plus tard, après avoir commis tous ces excès, c’est à moi qu’elle reviendra… Elle n’est pas revenue! Et sa perfide soeur, la nation de Juda, en a été témoin.
Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi.
8 Elle a vu que c’est bien à cause de son adultère que je l’avais répudiée, la nation renégate, Israël, et que je lui avais remis l’acte de divorce; mais sa soeur perfide, la nation de Juda, n’a pas pris peur; à son tour, elle alla se prostituer.
Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo.
9 Ses scandaleux dérèglements déshonorèrent le pays, elle trahit sa foi avec des idoles de pierre et de bois.
Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo.
10 Et malgré tout, sa perfide soeur, la nation de Juda, n’est pas revenue à moi de tout son coeur, mais de façon hypocrite," dit l’Eternel.
Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.
11 L’Eternel me dit encore: "La nation renégate d’Israël peut se prétendre innocente en comparaison de Juda, la nation perfide.
Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda.
12 Tu iras donc proclamer les paroles suivantes du côté du Nord, tu diras: Reviens, renégate, ô Israël! dit l’Eternel. Je ne ferai plus tomber mon courroux sur vous, car je suis clément, dit l’Eternel, mon ressentiment n’est pas durable.
Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti, “‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale, pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
13 Seulement, reconnais ta faute, que tu as péché contre l’Eternel, ton Dieu, que tu étais prodigue de démarches auprès des étrangers, sous tous les arbres verdoyants, et que tu n’écoutais pas ma voix", dit l’Eternel.
Ungovomera kulakwa kwako kuti unawukira Yehova Mulungu wako. Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndiponso kuti sunandimvere,’” akutero Yehova.
14 Revenez, enfants rebelles, dit l’Eternel, car je veux, moi, contracter une union avec vous. Je vous prendrai un par ville; deux par famille, et je vous amènerai à Sion.
“Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.
15 Je vous donnerai des pasteurs selon mon coeur, qui vous conduiront avec sagesse et discernement.
Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha.
16 Alors, quand vous serez devenus, à cette époque, nombreux et prospères dans le pays, déclare l’Eternel, on ne dira plus: Arche de l’Alliance du Seigneur! La pensée n’en reviendra plus à l’esprit, on n’en rappellera plus le souvenir ni on n’en remarquera l’absence: on n’en fera plus d’autre.
Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova.
17 En ces temps on appellera Jérusalem: "Trône de l’Eternel. Tous les peuples s’assembleront là, à Jérusalem, en l’honneur de l’Eternel, et ils cesseront de suivre les mauvais penchants de leur coeur.
Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa.
18 A cette époque, la maison de Juda ira se joindre à la maison d’Israël, et ensemble elles reviendront du pays du Nord au pays que j’ai donné comme héritage à vos ancêtres.
Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
19 Et je pensais en moi-même: "Comme je veux te faire une place parmi mes enfants et te donner un pays de délices, un patrimoine, magnifique entre tous, parmi les nations!" Et j’ajoutais: "Tu m’appelleras "mon Père" et tu ne t’éloigneras plus de moi."
“Ine mwini ndinati, “‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga ndikukupatsani dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’ Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ ndi kuti simudzaleka kunditsata.
20 Cependant, comme une épouse qui trahit son compagnon, ainsi vous m’avez trahi, maison d’Israël, dit l’Eternel.
Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake, momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,” akutero Yehova.
21 On entend du bruit sur les hauteurs: ce sont les sanglots, les supplications des enfants d’Israël! Car leur conduite a été dépravée, ils ont oublié l’Eternel, leur Dieu.
Mawu akumveka pa magomo, Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo chifukwa anatsata njira zoyipa ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.
22 Revenez, ô enfants rebelles! Je guérirai vos égarements. Nous voici, nous allons à toi, car tu es l’Eternel, notre Dieu.
Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika; ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.” “Inde, tidzabwerera kwa Inu pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
23 A coup sûr, ce n’était que mensonge ce qui venait des collines, ces attroupements dans les montagnes! à coup sûr, c’est en l’Eternel, notre Dieu, qu’est le salut d’Israël!
Ndithu kupembedza pa magomo komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu. Zoonadi chipulumutso cha Israeli chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
24 Et c’est ce culte honteux qui a dévoré, dès notre jeunesse, le fruit du labeur de nos pères, leurs brebis et leurs boeufs, leurs fils et leurs filles!
Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu la ntchito za makolo athu, nkhosa ndi ngʼombe zawo, ana awo aamuna ndi aakazi.
25 Couchons-nous dans notre honte, enveloppons-nous de notre ignominie, puisque nous avons péché contre l’Eternel, notre Dieu, nous et nos ancêtres, dès notre jeune âge et jusqu’à ce jour, faute d’écouter la voix de l’Eternel, notre Dieu.
Tilekeni tigone pansi mwa manyazi, ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe. Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu, ife pamodzi ndi makolo athu kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”

< Jérémie 3 >