< Salme 123 >
1 (Sang til Festrejserne.) Jeg løfter mine Øjne til dig, som troner i Himlen!
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
2 Som trælles øjne følger deres Herres Hånd, som en Trælkvindes Øjne følger hendes Frues Hånd, så følger vore Øjne HERREN vor Gud, til han er os nådig.
Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo.
3 Forbarm dig over os, HERRE, forbarm dig! Thi overmætte er vi af Spot,
Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu.
4 overmæt er vor Sjæl af de sorgløses Hån, de stoltes Spot!
Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.