< Josua 7 >

1 Men Israeliterne forgreb sig på det bandlyste, idet Akan, en Søn af Karmi en Søn af Zabdi, en Søn af Zera, af Judas Stamme, tilvendte sig noget af det bandlyste. Da blussede HERRENs Vrede op mod Israeliterne.
Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri.
2 Derpå sendte Josua nogle Mænd fra Jeriko til Aj, som ligger ved Bet Aven, østen for Betel, og sagde til dem: "Drag op og udspejd Egnen!" Og Mændene drog op og udspejdede Aj.
Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai.
3 Da de kom tilbage til Josua, sagde de til ham: "Lad ikke hele Folket drage derop; lad en to-tre Tusind Mand drage op og indtage Aj; du behøver ikke at umage hele Folket med at drage derop, thi de er få!"
Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.”
4 Så drog henved 3000 Mand af Folket derop; men de blev slået på Flugt af Ajjiterne,
Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai.
5 og Ajjiterne dræbte seks og tredive Mand eller så af dem; de forfulgte dem uden for Porten indtil Stenbruddene og huggede dem ned på Skråningen. Da sank Folkets Mod og blev til Vand.
Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.
6 Men Josua og Israels Ældste sønderrev deres Klæder og faldt på deres Ansigt på Jorden foran HERRENs Ark og blev liggende til Aften og kastede Støv på deres Hoveder.
Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo.
7 Og Josua sagde: "Ak, Herre, HERRE! Hvorfor lod du dette Folk gå over Jordan, når du vilde give os i Amoriternes Hånd og lade os gå til Grunde? Havde vi dog blot besluttet os til at blive hinsides Jordan!
Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani!
8 Ak, Herre! Hvad skal jeg sige, nu Israel har måttet tage Flugten for sine Fjender?
Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake?
9 Når Kana'anæerne og alle Landets Indbyggere hører det, falder de over os fra alle Sider og udsletter vort Navn af Jorden; hvad vil du da gøre for dit store Navns Skyld?"
Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”
10 Da sagde HERREN til Josua: "Stå op! Hvorfor ligger du på dit Ansigt?
Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?
11 Israel har syndet, thi de har forbrudt sig imod min Pagt, som jeg pålagde dem; de har tilvendt sig noget af det bandlyste, de har stjålet; de har skjult det, de har gemt det i deres Oppakning.
Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo.
12 Derfor kan Israeliterne ikke holde Stand over for deres Fjender, men må flygte for dem; thi de er hjemfaldne til Band! Jeg vil ikke mere være med eder, hvis I ikke bortrydder Bandet af eders Midte.
Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu.
13 Stå derfor op, lad Folket hellige sig og sig: Helliger eder til i Morgen, thi så siger HERREN, Israels Gud: Der er Band i din Midte, Israel; og du kan ikke holde Stand over for dine Fjender, før I skaffer Bandet bort fra eder!
“Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’
14 I Morgen skal I træde frem Stamme for Stamme, og den Stamme, HERREN rammer, skal træde frem Slægt for Slægt, og den Slægt, HERREN rammer, skal træde frem Familie for Familie, og den Familie, HERREN rammer, skal træde frem Mand for Mand.
“Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi.
15 Den, som da rammes, fordi han har det bandlyste Gods, skal brændes tillige med alt, hvad der tilhører ham; thi han har brudt HERRENs Pagt og begået en Skændselsdåd i Israel!"
Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!”
16 Tidligt næste Morgen lod Josua Israel træde frem Stamme for Stamme, og da blev Judas Stamme ramt.
Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa.
17 Derpå lod han Judas Slægter træde frem, og Zeraiternes Slægt blev ramt. Derpå lod han Zeraiternes Slægt træde frem Familie for Familie, og Zabdi blev ramt.
Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa.
18 Derpå lod han dennes Familie træde frem Mand for Mand, og da blev Akan ramt, en Søn af Harmi, en Søn af Zabdi, en Søn af Zera, af Judas Stamme.
Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda.
19 Da sagde Josua til Akan: "Min Søn, giv HERREN, Israels Gud, Ære og Pris, og fortæl mig, hvad du har gjort, skjul ikke noget for mig!"
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”
20 Akan svarede Josua: "Ja, det er mig, som har syndet mod HERREN, Israels Gud. Således gjorde jeg:
Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi:
21 Jeg så imellem Byttet en prægtig babylonisk Kappe, 200 Sekel Sølv og en Guldtunge på halvtredsindstyve Sekel; det fik jeg Lyst til, og jeg tog det; se, det ligger nedgravet i Jorden midt i mit Telt, Sølvet nederst."
Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.”
22 Da sendte Josua nogle Folk hen, og de skyndte sig til Teltet, og se, det var gemt i hans Telt, Sølvet nederst;
Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake.
23 og de tog det ud af Teltet og bragte det til Josua og alle Israeliterne og lagde det hen foran HERREN.
Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova.
24 Men Josua tog sammen med hele Israel Akan, Zeras Søn, og Sølvet, Kappen og Guldtungen og hans Sønner og Døtre, hans Hornkvæg, Æsler og Småkvæg, hans Telt og alt, hvad der tilhørte ham, og førte dem op i Akors dal.
Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori.
25 Og Josua sagde: "Hvorfor har du styrtet os i Ulykke? HERREN skal styrte dig i Ulykke på denne Dag!" Derpå stenede hele Israel ham, og de brændte eller stenede dem.
Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo.
26 Og de opkastede en stor Stendysse over ham, som står der den Dag i Dag. Da lagde HERRENs heftige Vrede sig. Derfor fik Stedet Navnet Akors Dal, som det hedder den Dag i Dag.
Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake.

< Josua 7 >