< 诗篇 122 >
1 大卫上行之诗。 人对我说:我们往耶和华的殿去, 我就欢喜。
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”
Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu.
Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda umene uli wothithikana pamodzi.
4 众支派,就是耶和华的支派,上那里去, 按以色列的常例称赞耶和华的名。
Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova.
5 因为在那里设立审判的宝座, 就是大卫家的宝座。
Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.
6 你们要为耶路撒冷求平安! 耶路撒冷啊,爱你的人必然兴旺!
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.
Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”
8 因我弟兄和同伴的缘故,我要说: 愿平安在你中间!
Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”
Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino.