< Masalimo 60 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere. Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
O Elohim, thou hast cast us off, thou hast scattered us, thou hast been displeased; O turn thyself to us again.
2 Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
Thou hast made the earth to tremble; thou hast broken it: heal the breaches thereof; for it shaketh.
3 Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto; inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.
Thou hast shewed thy people hard things: thou hast made us to drink the wine of astonishment.
4 Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta.
Thou hast given a banner to them that fear thee, that it may be displayed because of the truth. (Selah)
5 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
That thy beloved may be delivered; save with thy right hand, and hear me.
6 Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
Elohim hath spoken in his holiness; I will rejoice, I will divide Shechem, and mete out the valley of Succoth.
7 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
Gilead is mine, and Manasseh is mine; Ephraim also is the strength of mine head; Judah is my lawgiver;
8 Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”
Moab is my washpot; over Edom will I cast out my shoe: Philistia, triumph thou because of me.
9 Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
Who will bring me into the strong city? who will lead me into Edom?
10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
Wilt not thou, O Elohim, which hadst cast us off? and thou, O Elohim, which didst not go out with our armies?
11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu, pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
Give us help from trouble: for vain is the help of man.
12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano ndipo tidzapondaponda adani athu.
Through Elohim we shall do valiantly: for he it is that shall tread down our enemies.