Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Psalms Chapter 60 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Psalms/60 1) Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere. Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale! 2) Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri. 3) Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto; inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira. 4) Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta. 5) Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe. 6) Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti. 7) Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu 8) Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.” 9) Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu? 10) Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo. 11) Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu, pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu. 12) Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano ndipo tidzapondaponda adani athu. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!