< Masalimo 32 >

1 Salimo la Davide. Malangizo. Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.
לדוד משכיל אשרי נשוי-פשע כסוי חטאה
2 Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
אשרי אדם--לא יחשב יהוה לו עון ואין ברוחו רמיה
3 Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
כי-החרשתי בלו עצמי-- בשאגתי כל-היום
4 Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. (Sela)
כי יומם ולילה-- תכבד עלי ידך נהפך לשדי-- בחרבני קיץ סלה
5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” (Sela)
חטאתי אודיעך ועוני לא-כסיתי-- אמרתי אודה עלי פשעי ליהוה ואתה נשאת עון חטאתי סלה
6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza.
על-זאת יתפלל כל-חסיד אליך-- לעת מצא רק לשטף מים רבים-- אליו לא יגיעו
7 Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. (Sela)
אתה סתר לי-- מצר תצרני רני פלט תסובבני סלה
8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
אשכילך ואורך--בדרך-זו תלך איעצה עליך עיני
9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
אל-תהיו כסוס כפרד-- אין הבין במתג-ורסן עדיו לבלום בל קרב אליך
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
רבים מכאובים לרשע והבוטח ביהוה--חסד יסובבנו
11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
שמחו ביהוה וגילו צדיקים והרנינו כל-ישרי-לב

< Masalimo 32 >