< Masalimo 138 >

1 Salimo la Davide. Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
לדוד אודך בכל-לבי נגד אלהים אזמרך
2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.
אשתחוה אל-היכל קדשך ואודה את-שמך-- על-חסדך ועל-אמתך כי-הגדלת על-כל-שמך אמרתך
3 Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
ביום קראתי ותענני תרהבני בנפשי עז
4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu.
יודוך יהוה כל-מלכי-ארץ כי שמעו אמרי-פיך
5 Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
וישירו בדרכי יהוה כי-גדול כבוד יהוה
6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
כי-רם יהוה ושפל יראה וגבה ממרחק יידע
7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
אם-אלך בקרב צרה-- תחיני על אף איבי תשלח ידך ותושיעני ימינך
8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.
יהוה יגמר בעדי יהוה חסדך לעולם מעשי ידיך אל-תרף

< Masalimo 138 >