< Miyambo 8 >

1 Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
numquid non sapientia clamitat et prudentia dat vocem suam
2 Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu.
in summis excelsisque verticibus super viam in mediis semitis stans
3 Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti,
iuxta portas civitatis in ipsis foribus loquitur dicens
4 Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse.
o viri ad vos clamito et vox mea ad filios hominum
5 Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
intellegite parvuli astutiam et insipientes animadvertite
6 Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
audite quoniam de rebus magnis locutura sum et aperientur labia mea ut recta praedicent
7 Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
veritatem meditabitur guttur meum et labia mea detestabuntur impium
8 Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
iusti sunt omnes sermones mei non est in eis pravum quid neque perversum
9 Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
recti sunt intellegentibus et aequi invenientibus scientiam
10 Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
accipite disciplinam meam et non pecuniam doctrinam magis quam aurum eligite
11 Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.
melior est enim sapientia cunctis pretiosissimis et omne desiderabile ei non potest conparari
12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
ego sapientia habito in consilio et eruditis intersum cogitationibus
13 Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
timor Domini odit malum arrogantiam et superbiam et viam pravam et os bilingue detestor
14 Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
meum est consilium et aequitas mea prudentia mea est fortitudo
15 Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
per me reges regnant et legum conditores iusta decernunt
16 Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
per me principes imperant et potentes decernunt iustitiam
17 Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
ego diligentes me diligo et qui mane vigilant ad me invenient me
18 Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
mecum sunt divitiae et gloria opes superbae et iustitia
19 Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
melior est fructus meus auro et pretioso lapide et genimina mea argento electo
20 Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
in viis iustitiae ambulo in medio semitarum iudicii
21 Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.
ut ditem diligentes me et thesauros eorum repleam
22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
Dominus possedit me initium viarum suarum antequam quicquam faceret a principio
23 Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
ab aeterno ordita sum et ex antiquis antequam terra fieret
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
necdum erant abyssi et ego iam concepta eram necdum fontes aquarum eruperant
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
necdum montes gravi mole constiterant ante colles ego parturiebar
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
adhuc terram non fecerat et flumina et cardines orbis terrae
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
quando praeparabat caelos aderam quando certa lege et gyro vallabat abyssos
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
quando aethera firmabat sursum et librabat fontes aquarum
29 pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
quando circumdabat mari terminum suum et legem ponebat aquis ne transirent fines suos quando adpendebat fundamenta terrae
30 Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
cum eo eram cuncta conponens et delectabar per singulos dies ludens coram eo omni tempore
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
ludens in orbe terrarum et deliciae meae esse cum filiis hominum
32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga.
nunc ergo filii audite me beati qui custodiunt vias meas
33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga.
audite disciplinam et estote sapientes et nolite abicere eam
34 Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa.
beatus homo qui audit me qui vigilat ad fores meas cotidie et observat ad postes ostii mei
35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima.
qui me invenerit inveniet vitam et hauriet salutem a Domino
36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.”
qui autem in me peccaverit laedet animam suam omnes qui me oderunt diligunt mortem

< Miyambo 8 >