< Miyambo 18 >

1 Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha; iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.
Occasiones quaerit qui vult recedere ab amico: omni tempore erit exprobrabilis.
2 Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.
Non recipit stultus verba prudentiae: nisi ea dixeris quae versantur in corde eius.
3 Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera. Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.
Impius, cum in profundum venerit peccatorum, contemnit: sed sequitur eum ignominia et opprobrium.
4 Mawu a munthu ali ngati madzi akuya, kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.
Aqua profunda verba ex ore viri: et torrens redundans fons sapientiae.
5 Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu; kapena kupondereza munthu wosalakwa.
Accipere personam impii in iudicio non est bonum, ut declines a veritate iudicii.
6 Mawu a chitsiru amautsa mkangano; pakamwa pake pamayitana mkwapulo.
Labia stulti miscent se rixis: et os eius iurgia provocat.
7 Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake, ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.
Os stulti contritio eius: et labia ipsius, ruina animae eius.
8 Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma; amalowa mʼmimba mwa munthu.
Verba bilinguis, quasi simplicia: et ipsa perveniunt usque ad interiora ventris. Pigrum deiicit timor: animae autem effeminatorum esurient.
9 Munthu waulesi pa ntchito yake ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.
Qui mollis et dissolutus est in opere suo, frater est sua opera dissipantis.
10 Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.
Turris fortissima, nomen Domini: ad ipsam currit iustus, et exaltabitur.
11 Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba; chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.
Substantia divitis urbs roboris eius, et quasi murus validus circumdans eum.
12 Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
Antequam conteratur, exaltatur cor hominis: et antequam glorificetur, humiliatur.
13 Ukayankha usanamvetse bwino nkhani, umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.
Qui prius respondet quam audiat, stultum se esse demonstrat, et confusione dignum.
14 Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda, koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.
Spiritus viri sustentat imbecillitatem suam: spiritum vero ad irascendum facilem quis poterit sustinere?
15 Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina; amafunafuna kudziwa bwino zinthu.
Cor prudens possidebit scientiam: et auris sapientium quaerit doctrinam.
16 Mphatso ya munthu imamutsekulira njira yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.
Donum hominis dilatat viam eius, et ante principes spatium ei facit.
17 Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.
Iustus, prior est accusator sui: venit amicus eius, et investigabit eum.
18 Kuchita maere kumathetsa mikangano; amalekanitsa okangana amphamvu.
Contradictiones comprimit sors, et inter potentes quoque diiudicat.
19 Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.
Frater, qui adiuvatur a fratre, quasi civitas firma: et iudicia quasi vectes urbium.
20 Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake. Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.
De fructu oris viri replebitur venter eius: et genimina labiorum ipsius saturabunt eum.
21 Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.
Mors, et vita in manu linguae: qui diligunt eam, comedent fructus eius.
22 Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.
Qui invenit mulierem bonam, invenit bonum: et hauriet iucunditatem a Domino. Qui expellit mulierem bonam, expellit bonum: qui autem tenet adulteram, stultus est et insipiens.
23 Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali.
Cum obsecrationibus loquitur pauper: et dives effabitur rigide.
24 Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.
Vir amicabilis ad societatem, magis amicus erit, quam frater.

< Miyambo 18 >