< Nahumu 1 >

1 Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.
משא נינוה--ספר חזון נחום האלקשי
2 Yehova ndi Mulungu wansanje ndiponso wobwezera; Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. Yehova amabwezera adani ake ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.
אל קנוא ונקם יהוה נקם יהוה ובעל חמה נקם יהוה לצריו ונוטר הוא לאיביו
3 Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
יהוה ארך אפים וגדול (וגדל) כח ונקה לא ינקה יהוה בסופה ובשערה דרכו וענן אבק רגליו
4 Amalamulira nyanja ndipo imawuma; amawumitsa mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota.
גוער בים ויבשהו וכל הנהרות החריב אמלל בשן וכרמל ופרח לבנון אמלל
5 Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.
הרים רעשו ממנו והגבעות התמגגו ותשא הארץ מפניו ותבל וכל יושבי בה
6 Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake.
לפני זעמו מי יעמוד ומי יקום בחרון אפו חמתו נתכה כאש והצרים נתצו ממנו
7 Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,
טוב יהוה למעוז ביום צרה וידע חסי בו
8 koma ndi madzi achigumula choopsa Iye adzawononga adani ake (Ninive); adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima.
ובשטף עבר כלה יעשה מקומה ואיביו ירדף חשך
9 Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova adzachiwononga kotheratu; msautso sudzabweranso kachiwiri.
מה תחשבון אל יהוה--כלה הוא עשה לא תקום פעמים צרה
10 Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.
כי עד סירים סבכים וכסבאם סבואים אכלו--כקש יבש מלא
11 Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, wofuna kuchitira Yehova chiwembu, amene amapereka uphungu woyipa.
ממך יצא חשב על יהוה רעה--יעץ בליעל
12 Yehova akuti, “Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, kaya iwowo ndi ambiri, koma adzawonongedwa ndi kutheratu. Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, sindidzakuzunzanso.
כה אמר יהוה אם שלמים וכן רבים וכן נגוזו ועבר וענתך--לא אענך עוד
13 Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako ndipo ndidzadula maunyolo ako.”
ועתה אשבר מטהו מעליך ומוסרתיך אנתק
14 Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, “Sudzakhala ndi zidzukulu zimene zidzadziwike ndi dzina lako. Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba amene ali mʼnyumba ya milungu yako. Ine ndidzakukumbira manda chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
וצוה עליך יהוה לא יזרע משמך עוד מבית אלהיך אכרית פסל ומסכה אשים קברך--כי קלות
15 Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu.
הנה על ההרים רגלי מבשר משמיע שלום--חגי יהודה חגיך שלמי נדריך כי לא יוסיף עוד לעבור (לעבר) בך בליעל כלה נכרת

< Nahumu 1 >