Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Nahum Chapter 1 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Nahum/1 1) Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi. 2) Yehova ndi Mulungu wansanje ndiponso wobwezera; Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. Yehova amabwezera adani ake ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo. 3) Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake. 4) Amalamulira nyanja ndipo imawuma; amawumitsa mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota. 5) Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo. 6) Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake. 7) Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira, 8) koma ndi madzi achigumula choopsa Iye adzawononga adani ake (Ninive); adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima. 9) Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova adzachiwononga kotheratu; msautso sudzabweranso kachiwiri. 10) Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; adzatenthedwa ngati ziputu zowuma. 11) Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, wofuna kuchitira Yehova chiwembu, amene amapereka uphungu woyipa. 12) Yehova akuti, “Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, kaya iwowo ndi ambiri, koma adzawonongedwa ndi kutheratu. Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, sindidzakuzunzanso. 13) Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako ndipo ndidzadula maunyolo ako.” 14) Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, “Sudzakhala ndi zidzukulu zimene zidzadziwike ndi dzina lako. Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba amene ali mʼnyumba ya milungu yako. Ine ndidzakukumbira manda chifukwa ndiwe woyipitsitsa.” 15) Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!