< Luka 24 >
1 Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda.
But on the first day of the week, at early dawn, they came to the tomb, bringing the spices which they had prepared.
2 Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika
They found the stone rolled away from the tomb.
3 ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.
They entered in, and did not find the body of the Lord Jesus.
4 Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo.
It happened, while they were greatly perplexed about this, look, two men stood by them in dazzling clothing.
5 Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa?
Becoming terrified, they bowed their faces down to the earth. They said to them, "Why do you seek the living among the dead?
6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:
He is not here, but is risen. Remember what he told you when he was still in Galilee,
7 ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’”
saying that the Son of Man must be delivered up into the hands of sinful men, and be crucified, and the third day rise again?"
8 Ndipo anakumbukira mawu ake.
Then they remembered his words.
9 Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse.
And returning from the tomb, they told all these things to the eleven and to all the rest.
10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi.
Now they were Mary Magdalene and Joanna and Mary the mother of James and the other women with them who told these things to the apostles.
11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru.
These words seemed to them to be nonsense, and they did not believe them.
12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
But Peter got up and ran to the tomb. Stooping and looking in, he saw the strips of linen by themselves, and he departed to his home, wondering what had happened.
13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu.
And look, two of them were going that very day to a village named Emmaus, which was about seven miles from Jerusalem.
14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo.
They talked with each other about all of these things which had happened.
15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi;
It happened, while they talked and questioned together, that Jesus himself came near, and went with them.
16 koma iwo sanamuzindikire.
But their eyes were kept from recognizing him.
17 Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa.
And he said to them, "What are these words that you are exchanging with each other as you walk?" And they stood still, looking sad.
18 Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?”
One of them, named Cleopas, answered him, "Are you the only stranger in Jerusalem who does not know the things which have happened there in these days?"
19 Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
He said to them, "What things?" They said to him, "The things concerning Jesus, the Nazarene, a man who was a prophet mighty in deed and word before God and all the people;
20 Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye;
and how the chief priests and our rulers delivered him up to be condemned to death, and crucified him.
21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi.
But we were hoping that it was he who would redeem Israel. Yes, and besides all this, it is now the third day since these things happened.
22 Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa
Also, certain women of our company amazed us, having arrived early at the tomb;
23 koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo.
and when they did not find his body, they came saying that they had also seen a vision of angels, who said that he was alive.
24 Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.”
Some of us went to the tomb, and found it just like the women had said, but they did not see him."
25 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!
Then he said to them, "O foolish ones, and slow of heart to believe in all that the prophets have spoken.
26 Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?”
Did not the Christ have to suffer these things and to enter into his glory?"
27 Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
Beginning from Moses and from all the prophets, he explained to them in all the Scriptures the things concerning himself.
28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira.
They drew near to the village, where they were going, and he acted like he would go further.
29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
They urged him, saying, "Stay with us, for it is almost evening, and the day is almost over." He went in to stay with them.
30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira.
It happened, that when he had sat down at the table with them, he took the bread and gave thanks. Breaking it, he gave to them.
31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo.
Their eyes were opened, and they recognized him, and he vanished out of their sight.
32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
And they said to one another, "Weren't our hearts burning within us, while he spoke to us along the way, and while he opened the Scriptures to us?"
33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi
They rose up that very hour, returned to Jerusalem, and found the eleven gathered together, and those who were with them,
34 ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.”
saying, "The Lord is risen indeed, and has appeared to Simon."
35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
They related the things that happened along the way, and how he was recognized by them in the breaking of the bread.
36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”
As they said these things, Jesus himself stood among them, and said to them, "Peace be to you."
37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa.
But they were terrified and filled with fear, and supposed that they had seen a spirit.
38 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?
He said to them, "Why are you troubled? Why do doubts arise in your hearts?
39 Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
See my hands and my feet, that it is truly me. Touch me and see, for a spirit does not have flesh and bones, as you see that I have."
40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake.
When he had said this, he showed them his hands and his feet.
41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”
While they still did not believe for joy, and wondered, he said to them, "Do you have anything here to eat?"
42 Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika.
And they gave him a piece of a broiled fish.
43 Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.
And he took it and ate in front of them.
44 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
And he said to them, "This is what I told you, while I was still with you, that all things which are written in the Law of Moses, the Prophets, and the Psalms, concerning me must be fulfilled."
45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.
Then he opened their minds, that they might understand the Scriptures.
46 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu.
He said to them, "Thus it is written, for the Christ to suffer and to rise from the dead the third day,
47 Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
and that repentance leading to forgiveness of sins should be preached in his name to all the nations, beginning at Jerusalem.
48 Inu ndinu mboni za zimenezi.
You are witnesses of these things.
49 Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”
And look, I send forth the promise of my Father on you. But wait in the city until you are clothed with power from on high."
50 Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.
He led them out as far as Bethany, and he lifted up his hands, and blessed them.
51 Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba.
It happened, while he blessed them, that he departed from them, and was carried up into heaven.
52 Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
They worshiped him, and returned to Jerusalem with great joy,
53 Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.
and were continually in the temple, praising and blessing God.