< Yohane 8 >

1 Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi.
Iesus autem perrexit in montem Oliveti:
2 Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa.
et diluculo iterum venit in templum, et omnis populus venit ad eum, et sedens docebat eos.
3 Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo
Adducunt autem scribæ, et Pharisæi mulierem in adulterio deprehensam: et statuerunt eam in medio,
4 anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo.
et dixerunt ei: Magister, hæc mulier modo deprehensa est in adulterio.
5 Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?”
In lege autem Moyses mandavit nobis huiusmodi lapidare. Tu ergo quid dicis?
6 Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye. Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake.
Hoc autem dicebant tentantes eum, ut possent accusare eum. Iesus autem inclinans se deorsum, digito scribebat in terra.
7 Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.”
Cum ergo perseverarent interrogantes eum, erexit se, et dixit eis: Qui sine peccato est vestrum, primus in illam lapidem mittat.
8 Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
Et iterum se inclinans, scribebat in terra.
9 Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo.
Audientes autem unus post unum exibant, incipientes a senioribus: et remansit solus Iesus, et mulier in medio stans.
10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”
Erigens autem se Iesus, dixit ei: Mulier, ubi sunt, qui te accusabant? Nemo te condemnavit?
11 Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.” “Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
Quæ dixit: Nemo, Domine. Dixit autem Iesus: Nec ego te condemnabo: Vade, et iam amplius noli peccare.
12 Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
Iterum ergo locutus est eis Iesus, dicens: Ego sum lux mundi: qui sequitur me, non ambulat in tenebris, sed habebit lumen vitæ.
13 Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”
Dixerunt ergo ei Pharisæi: Tu de teipso testimonium perhibes: testimonium tuum non est verum.
14 Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita.
Respondit Iesus, et dixit eis: Et si ego testimonium perhibeo de meipso, verum est testimonium meum: quia scio unde veni, et quo vado: vos autem nescitis unde venio, aut quo vado.
15 Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense.
Vos secundum carnem iudicatis: ego non iudico quemquam:
16 Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma.
et si iudico ego, iudicium meum verum est, quia solus non sum: sed ego, et qui misit me, Pater.
17 Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka.
Et in lege vestra scriptum est, quia duorum hominum testimonium verum est.
18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”
Ego sum, qui testimonium perhibeo de me ipso: et testimonium perhibet de me, qui misit me, Pater.
19 Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?” Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.”
Dicebant ergo ei: Ubi est Pater tuus? Respondit Iesus: Neque me scitis, neque Patrem meum: si me sciretis, forsitan et Patrem meum sciretis.
20 Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.
Hæc verba locutus est Iesus in gazophylacio, docens in templo: et nemo apprehendit eum, quia necdum venerat hora eius.
21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”
Dixit ergo iterum eis Iesus: Ego vado, et quæretis me, et in peccato vestro moriemini. Quo ego vado, vos non potestis venire.
22 Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’”
Dicebant ergo Iudæi: Numquid interficiet semetipsum, quia dixit: Quo ego vado, vos non potestis venire?
23 Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino.
Et dicebat eis: Vos de deorsum estis, ego de supernis sum. Vos de mundo hoc estis, ego non sum de hoc mundo.
24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”
Dixi ergo vobis quia moriemini in peccatis vestris: si enim non credideritis quia ego sum, moriemini in peccato vestro.
25 Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?” Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi,
Dicebant ergo ei: Tu quis es? Dixit eis Iesus: Principium, qui et loquor vobis.
26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
Multa habeo de vobis loqui, et iudicare. Sed qui me misit, verax est: et ego quæ audivi ab eo, hæc loquor in mundo.
27 Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake.
Et non cognoverunt quia Patrem eius dicebat Deum.
28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa.
Dixit ergo eis Iesus: Cum exaltaveritis Filium hominis, tunc cognoscetis quia ego sum, et a meipso facio nihil, sed sicut docuit me Pater, hæc loquor:
29 Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.”
et qui me misit, mecum est, et non reliquit me solum: quia ego quæ placita sunt ei, facio semper.
30 Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.
Hæc illo loquente, multi crediderunt in eum.
31 Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga.
Dicebat ergo Iesus ad eos, qui crediderunt ei, Iudæos: Si vos manseritis in sermone meo, vere discipuli mei eritis:
32 Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
et cognoscetis veritatem, et veritas liberabit vos.
33 Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’”
Responderunt ei: Semen Abrahæ sumus, et nemini servivimus umquam: quomodo tu dicis: Liberi eritis?
34 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.
Respondit eis Iesus: Amen, amen dico vobis: quia omnis, qui facit peccatum, servus est peccati.
35 Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. (aiōn g165)
Servus autem non manet in domo in æternum: Filius autem manet in æternum. (aiōn g165)
36 Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu.
Si ergo vos Filius liberaverit, vere liberi eritis.
37 Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu.
Scio quia filii Abrahæ estis: sed quæritis me interficere, quia sermo meus non capit in vobis.
38 Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”
Ego quod vidi apud Patrem meum, loquor: et vos quæ vidistis apud patrem vestrum, facitis.
39 Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.” Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita.
Responderunt, et dixerunt ei: Pater noster Abraham est. Dicit eis Iesus: Si filii Abrahæ estis, opera Abrahæ facite.
40 Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi.
Nunc autem quæritis me interficere, hominem, qui veritatem vobis locutus sum, quam audivi a Deo: hoc Abraham non fecit.
41 Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.” Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”
Vos facitis opera patris vestri. Dixerunt itaque ei: Nos ex fornicatione non sumus nati: unum patrem habemus Deum.
42 Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha.
Dixit ergo eis Iesus: Si Deus pater vester esset: diligeretis utique et me. Ego enim ex Deo processi, et veni: neque enim a me ipso veni, sed ille me misit.
43 Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga.
Quare loquelam meam non cognoscitis? Quia non potestis audire sermonem meum.
44 Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.
Vos ex patre diabolo estis: et desideria patris vestri vultis facere. Ille homicida erat ab initio, et in veritate non stetit: quia non est veritas in eo: cum loquitur mendacium, ex propriis loquitur, quia mendax est, et pater eius.
45 Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine!
Ego autem si veritatem dico, non creditis mihi.
46 Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira?
Quis ex vobis arguet me de peccato? Si veritatem dico vobis, quare non creditis mihi?
47 Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”
Qui ex Deo est, verba Dei audit. Propterea vos non auditis, quia ex Deo non estis.
48 Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”
Responderunt ergo Iudæi, et dixerunt ei: Nonne bene dicimus nos quia Samaritanus es tu, et dæmonium habes?
49 Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza.
Respondit Iesus: Ego dæmonium non habeo: sed honorifico Patrem meum, et vos inhonorastis me.
50 Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza.
Ego autem non quæro gloriam meam: est qui quærat, et iudicet.
51 Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.” (aiōn g165)
Amen, amen dico vobis: si quis sermonem meum servaverit, mortem non videbit in æternum. (aiōn g165)
52 Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’ (aiōn g165)
Dixerunt ergo Iudæi: Nunc cognovimus quia dæmonium habes. Abraham mortuus est, et Prophetæ: et tu dicis: Si quis sermonem meum servaverit, non gustabit mortem in æternum. (aiōn g165)
53 Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”
Numquid tu maior es patre nostro Abraham, qui mortuus est? et Prophetæ mortui sunt. Quem te ipsum facis?
54 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine.
Respondit Iesus: Si ego glorifico me ipsum, gloria mea nihil est: est Pater meus, qui glorificat me, quem vos dicitis quia Deus vester est.
55 Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake.
Et non cognovistis eum: ego autem novi eum: Et si dixero quia non scio eum, ero similis vobis, mendax. Sed scio eum, et sermonem eius servo.
56 Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”
Abraham pater vester exultavit ut videret diem meum: vidit, et gavisus est.
57 Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”
Dixerunt ergo Iudæi ad eum: Quinquaginta annos nondum habes, et Abraham vidisti?
58 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!”
Dixit eis Iesus: Amen, amen dico vobis, antequam Abraham fieret, ego sum.
59 Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.
Tulerunt ergo lapides, ut iacerent in eum: Iesus autem abscondit se, et exivit de templo.

< Yohane 8 >