< Luka 1 >

1 Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu,
Quoniam quidem multi conati sunt ordinare narrationem, quæ in nobis completæ sunt, rerum:
2 monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu.
sicut tradiderunt nobis, qui ab initio ipsi viderunt, et ministri fuerunt sermonis:
3 Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo,
visum est et mihi, assecuto omnia a principio diligenter, ex ordine tibi scribere, optime Theophile,
4 kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.
ut cognoscas eorum verborum, de quibus eruditus es, veritatem.
5 Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni.
Fuit in diebus Herodis, regis Iudææ, sacerdos quidam nomine Zacharias de vice Abia, et uxor illius de filiabus Aaron, et nomen eius Elisabeth.
6 Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse.
Erant autem iusti ambo ante Deum, incedentes in omnibus mandatis, et iustificationibus Domini sine querela:
7 Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba.
Et non erat illis filius eo quod esset Elisabeth sterilis, et ambo processissent in diebus suis.
8 Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu,
Factum est autem, cum sacerdotio fungeretur in ordine vicis suæ ante Deum,
9 Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani.
secundum consuetudinem sacerdotii, sorte exiit ut incensum poneret, ingressus in templum Domini:
10 Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja.
et omnis multitudo populi erat orans foris hora incensi.
11 Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira.
Apparuit autem illi Angelus Domini, stans a dextris altaris incensi.
12 Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha.
Et Zacharias turbatus est videns, et timor irruit super eum.
13 Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane.
Ait autem ad illum Angelus: Ne timeas Zacharia, quoniam exaudita est deprecatio tua: et uxor tua Elisabeth pariet tibi filium, et vocabis nomen eius Ioannem:
14 Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake,
et erit gaudium tibi, et exultatio, et multi in nativitate eius gaudebunt:
15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa.
erit enim magnus coram Domino: et vinum, et siceram non bibet, et Spiritu Sancto replebitur adhuc ex utero matris suæ:
16 Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo.
et multos filiorum Israel convertet ad Dominum Deum ipsorum:
17 Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”
et ipse præcedet ante illum in spiritu, et virtute Eliæ: ut convertat corda patrum in filios, et incredulos ad prudentiam iustorum, parare Domino plebem perfectam.
18 Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”
Et dixit Zacharias ad Angelum: Unde hoc sciam? Ego enim sum senex, et uxor mea processit in diebus suis.
19 Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu.
Et respondens Angelus dixit ei: Ego sum Gabriel, qui asto ante Deum: et missus sum loqui ad te, et hæc tibi evangelizare.
20 Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
Et ecce eris tacens, et non poteris loqui usque in diem, quo hæc fiant, pro eo quod non credidisti verbis meis, quæ implebuntur in tempore suo.
21 Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu.
Et erat plebs expectans Zachariam: et mirabantur quod tardaret ipse in templo.
22 Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.
Egressus autem non poterat loqui ad illos, et cognoverunt quod visionem vidisset in templo. Et ipse erat innuens illis, et permansit mutus.
23 Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo.
Et factum est, ut impleti sunt dies officii eius abiit in domum suam:
24 Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu.
post hos autem dies concepit Elisabeth uxor eius, et occultabat se mensibus quinque, dicens:
25 Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.”
Quia sic fecit mihi Dominus in diebus, quibus respexit auferre opprobrium meum inter homines.
26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya,
In mense autem sexto, missus est Angelus Gabriel a Deo in civitatem Galilææ, cui nomen Nazareth,
27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya.
ad Virginem desponsatam viro, cui nomen erat Ioseph, de domo David, et nomen virginis Maria.
28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”
Et ingressus Angelus ad eam dixit: Ave gratia plena: Dominus tecum: Benedicta tu in mulieribus.
29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere.
Quæ cum audisset, turbata est in sermone eius, et cogitabat qualis esset ista salutatio.
30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu.
Et ait Angelus ei: Ne timeas Maria, invenisti enim gratiam apud Deum.
31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu.
Ecce concipies in utero, et paries filium, et vocabis nomen eius IESUM.
32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide,
Hic erit magnus, et Filius Altissimi vocabitur, et dabit illi Dominus Deus sedem David patris eius:
33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.” (aiōn g165)
et regnabit in domo Iacob in æternum, et regni eius non erit finis. (aiōn g165)
34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”
Dixit autem Maria ad Angelum: Quomodo fiet istud, quoniam virum non cognosco?
35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.
Et respondens Angelus dixit ei: Spiritus Sanctus superveniet in te, et virtus Altissimi obumbrabit tibi. Ideoque et quod nascetur ex te Sanctum, vocabitur Filius Dei.
36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.
Et ecce Elisabeth cognata tua, et ipsa concepit filium in senectute sua: et hic mensis sextus est illi, quæ vocatur sterilis:
37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”
quia non erit impossibile apud Deum omne verbum.
38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”
Dixit autem Maria: Ecce ancilla Domini, fiat mihi secundum verbum tuum. Et discessit ab illa Angelus.
39 Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya,
Exurgens autem Maria in diebus illis abiit in montana cum festinatione, in civitatem Iuda:
40 kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti.
Et intravit in domum Zachariæ, et salutavit Elisabeth.
41 Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Et factum est, ut audivit salutationem Mariæ Elisabeth, exultavit infans in utero eius, et repleta est Spiritu Sancto Elisabeth:
42 Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke!
et exclamavit voce magna, et dixit: Benedicta tu inter mulieres, et benedictus fructus ventris tui.
43 Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine?
Et unde hoc mihi ut veniat mater Domini mei ad me?
44 Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe.
Ecce enim ut facta est vox salutationis tuæ in auribus meis, exultavit in gaudio infans in utero meo.
45 Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!”
Et beata, quæ credidisti, quoniam perficientur ea, quæ dicta sunt tibi a Domino.
46 Ndipo Mariya anati: “Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
Et ait Maria: Magnificat anima mea Dominum:
47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
et exultavit spiritus meus in Deo salutari meo.
48 pakuti wakumbukira kudzichepetsa kwa mtumiki wake. Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
Quia respexit humilitatem ancillæ suæ: ecce enim ex hoc beatam me dicent omnes generationes.
49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu, dzina lake ndi loyera.
Quia fecit mihi magna qui potens est: et sanctum nomen eius.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye kufikira mibadomibado.
Et misericordia eius a progenie in progenies timentibus eum.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake; Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
Fecit potentiam in brachio suo: dispersit superbos mente cordis sui.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, koma wakweza odzichepetsa.
Deposuit potentes de sede, et exaltavit humiles.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
Esurientes implevit bonis: et divites dimisit inanes.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, pokumbukira chifundo chake.
Suscepit Israel puerum suum, recordatus misericordiæ suæ.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse monga ananena kwa makolo athu.” (aiōn g165)
Sicut locutus est ad patres nostros, Abraham, et semini eius in sæcula. (aiōn g165)
56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo.
Mansit autem Maria cum illa quasi mensibus tribus: et reversa est in domum suam.
57 Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna.
Elisabeth autem impletum est tempus pariendi, et peperit filium.
58 Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi.
Et audierunt vicini, et cognati eius quia magnificavit Dominus misericordiam suam cum illa, et congratulabantur ei.
59 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya,
Et factum est in die octavo, venerunt circumcidere puerum, et vocabant eum nomine patris sui Zachariam.
60 koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.”
Et respondens mater eius, dixit: Nequaquam, sed vocabitur Ioannes.
61 Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.”
Et dixerunt ad illam: Quia nemo est in cognatione tua, qui vocetur hoc nomine.
62 Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo.
Innuebant autem patri eius, quem vellet vocari eum.
63 Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.”
Et postulans pugillarem scripsit, dicens: Ioannes est nomen eius. Et mirati sunt universi.
64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu.
Apertum est autem illico os eius, et lingua eius, et loquebatur benedicens Deum.
65 Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi.
Et factus est timor super omnes vicinos eorum: et super omnia montana Iudææ divulgabantur omnia verba hæc:
66 Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.
et posuerunt omnes, qui audierant in corde suo, dicentes: Quis, putas, puer iste erit? Etenim manus Domini erat cum illo.
67 Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,
Et Zacharias pater eius repletus est Spiritu Sancto: et prophetavit, dicens:
68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
Benedictus Dominus Deus Israel, quia visitavit, et fecit redemptionem plebis suæ:
69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
Et erexit cornu salutis nobis: in domo David pueri sui.
70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera), (aiōn g165)
Sicut locutum est per os sanctorum, qui a sæculo sunt, prophetarum eius: (aiōn g165)
71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
Salutem ex inimicis nostris, et de manu omnium, qui oderunt nos:
72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera,
Ad faciendam misericordiam cum patribus nostris: et memorari testamenti sui sancti.
73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
Iusiurandum, quod iuravit ad Abraham patrem nostrum, daturum se nobis:
74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu, ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
Ut sine timore, de manu inimicorum nostrorum liberati, serviamus illi.
75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.
In sanctitate, et iustitia coram ipso, omnibus diebus nostris.
76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba; pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
Et tu puer, propheta Altissimi vocaberis: præibis enim ante faciem Domini parare vias eius:
77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
Ad dandam scientiam salutis plebi eius: in remissionem peccatorum eorum:
78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
Per viscera misericordiæ Dei nostri: in quibus visitavit nos, oriens ex alto:
79 kuwalira iwo okhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa, kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”
Illuminare his, qui in tenebris, et in umbra mortis sedent: ad dirigendos pedes nostros in viam pacis.
80 Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.
Puer autem crescebat, et confortabatur spiritu: et erat in desertis usque in diem ostensionis suæ ad Israel.

< Luka 1 >