< Yobu 10 >

1 “Ine ndatopa nawo moyo wanga; choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.
I am weary of my life; I will let loose within me my complaint; I will speak in the bitterness of my soul.
2 Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa, koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.
I will say unto God, Do not condemn me! Show me wherefore thou contendest with me!
3 Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?
Is it a pleasure to thee to oppress, And to despise the work of thy hands, And to shine upon the plans of the wicked?
4 Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?
Hast thou eyes of flesh, Or seest thou as man seeth?
5 Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu, kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,
Are thy days as the days of a man, Are thy years as the days of a mortal,
6 kuti Inu mufufuze zolakwa zanga ndi kulondola tchimo langa,
That thou seekest after my iniquity, And searchest after my sin,
7 ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?
Though thou knowest that I am not guilty, And that none can deliver from thy hand?
8 “Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?
Have thy hands completely fashioned and made me In every part, that thou mightst destroy me?
9 Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
O remember that thou hast moulded me as clay! And wilt thou bring me again to dust?
10 Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?
Thou didst pour me out as milk, And curdle me as cheese;
11 Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?
With skin and flesh didst thou clothe me, And strengthen me with bones and sinews;
12 Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu, ndipo munasamalira bwino moyo wanga.
Thou didst grant me life and favor, And thy protection preserved my breath:
13 “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu, ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:
Yet these things thou didst lay up in thy heart! I know that this was in thy mind.
14 Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.
If I sin, then thou markest me, And wilt not acquit me of mine iniquity.
15 Ngati ndili wolakwa, tsoka langa! Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga, pakuti ndagwidwa ndi manyazi ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.
If I am wicked, —then woe unto me! Yet if righteous, I dare not lift up my head; I am full of confusion, beholding my affliction.
16 Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.
If I lift it up, like a lion thou huntest me, And again showest thyself terrible unto me.
17 Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.
Thou renewest thy witnesses against me, And increasest thine anger toward me; New hosts continually rise up against me.
18 “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe? Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.
Why then didst thou bring me forth from the womb? I should have perished, and no eye had seen me;
19 Ndikanapanda kubadwa, kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!
I should be as though I had not been; I should have been borne from the womb to the grave.
20 Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha? Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha
Are not my days few? O spare then, And let me alone, that I may be at ease a little while,
21 ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,
Before I go— whence I shall not return—To the land of darkness and death-shade,
22 ku dziko la mdima wandiweyani ndi chisokonezo, kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”
The land of darkness like the blackness of death-shade, Where is no order, and where the light is as darkness.

< Yobu 10 >