Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Job Chapter 10 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Job/10 1) “Ine ndatopa nawo moyo wanga; choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga. 2) Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa, koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine. 3) Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa? 4) Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu? 5) Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu, kapena zaka zanu ngati zaka za munthu, 6) kuti Inu mufufuze zolakwa zanga ndi kulondola tchimo langa, 7) ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu? 8) “Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga? 9) Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi? 10) Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga? 11) Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha? 12) Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu, ndipo munasamalira bwino moyo wanga. 13) “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu, ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu: 14) Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga. 15) Ngati ndili wolakwa, tsoka langa! Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga, pakuti ndagwidwa ndi manyazi ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga. 16) Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu. 17) Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira. 18) “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe? Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione. 19) Ndikanapanda kubadwa, kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda! 20) Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha? Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha 21) ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani, 22) ku dziko la mdima wandiweyani ndi chisokonezo, kumene kuwala kumakhala ngati mdima.” Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!