< Yeremiya 31 >

1 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
בעת ההיא נאם יהוה אהיה לאלהים לכל משפחות ישראל והמה יהיו לי לעם
2 Yehova akuti, “Anthu amene anapulumuka ku nkhondo ndinawakomera mtima mʼchipululu; pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”
כה אמר יהוה מצא חן במדבר עם שרידי חרב הלוך להרגיעו ישראל
3 Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
מרחוק יהוה נראה לי ואהבת עולם אהבתיך על כן משכתיך חסד
4 Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli; mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu, ndipo mudzapita kukavina nawo anthu ovina mwachimwemwe.
עוד אבנך ונבנית בתולת ישראל עוד תעדי תפיך ויצאת במחול משחקים
5 Mudzalimanso minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; alimi adzadzala mphesa ndipo adzadya zipatso zake.
עוד תטעי כרמים בהרי שמרון נטעו נטעים וחללו
6 Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula pa mapiri a Efereimu nati, ‘Tiyeni tipite ku Ziyoni, kwa Yehova Mulungu wathu.’”
כי יש יום קראו נצרים בהר אפרים קומו ונעלה ציון אל יהוה אלהינו
7 Yehova akuti, “Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo, fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Matamando anu amveke, ndipo munene kuti, ‘Yehova wapulumutsa anthu ake otsala a Israeli.’
כי כה אמר יהוה רנו ליעקב שמחה וצהלו בראש הגוים השמיעו הללו ואמרו הושע יהוה את עמך את שארית ישראל
8 Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto, ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi. Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
הנני מביא אותם מארץ צפון וקבצתים מירכתי ארץ--בם עור ופסח הרה וילדת יחדו קהל גדול ישובו הנה
9 Adzabwera akulira; koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza. Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo. Chifukwa ndine abambo ake a Israeli, ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.
בבכי יבאו ובתחנונים אובילם--אוליכם אל נחלי מים בדרך ישר לא יכשלו בה כי הייתי לישראל לאב ואפרים בכרי הוא
10 “Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina; lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja; ‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
שמעו דבר יהוה גוים והגידו באיים ממרחק ואמרו מזרה ישראל יקבצנו ושמרו כרעה עדרו
11 Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
כי פדה יהוה את יעקב וגאלו מיד חזק ממנו
12 Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni; adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova. Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta, ana ankhosa ndi ana angʼombe. Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino, ndipo sadzamvanso chisoni.
ובאו ורננו במרום ציון ונהרו אל טוב יהוה על דגן ועל תירש ועל יצהר ועל בני צאן ובקר והיתה נפשם כגן רוה ולא יוסיפו לדאבה עוד
13 Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala. Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala. Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo; ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
אז תשמח בתולה במחול ובחרים וזקנים יחדו והפכתי אבלם לששון ונחמתים ושמחתים מיגונם
14 Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,” akutero Yehova.
ורויתי נפש הכהנים דשן ועמי את טובי ישבעו נאם יהוה
15 Yehova akuti, “Kulira kukumveka ku Rama, kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake. Sakutonthozeka chifukwa ana akewo palibe.”
כה אמר יהוה קול ברמה נשמע נהי בכי תמרורים--רחל מבכה על בניה מאנה להנחם על בניה כי איננו
16 Yehova akuti, “Leka kulira ndi kukhetsa misozi pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,” akutero Yehova. “Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
כה אמר יהוה מנעי קולך מבכי ועיניך מדמעה כי יש שכר לפעלתך נאם יהוה ושבו מארץ אויב
17 Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,” akutero Yehova. “Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.
ויש תקוה לאחריתך נאם יהוה ושבו בנים לגבולם
18 “Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti, ‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva. Koma inu mwatiphunzitsa kumvera. Mutibweze kuti tithe kubwerera, chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
שמוע שמעתי אפרים מתנודד יסרתני ואוסר כעגל לא למד השבני ואשובה כי אתה יהוה אלהי
19 Popeza tatembenuka mtima, ndiye tikumva chisoni; popeza tazindikira ndiye tikudziguguda pachifukwa. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
כי אחרי שובי נחמתי ואחרי הודעי ספקתי על ירך בשתי וגם נכלמתי כי נשאתי חרפת נעורי
20 Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa, mwana amene Ine ndimakondwera naye? Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula, ndimamukumbukirabe. Kotero mtima wanga ukumufunabe; ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,” akutero Yehova.
הבן יקיר לי אפרים אם ילד שעשעים--כי מדי דברי בו זכר אזכרנו עוד על כן המו מעי לו--רחם ארחמנו נאם יהוה
21 “Muyike zizindikiro za mu msewu; muyimike zikwangwani. Yangʼanitsitsani msewuwo, njira imene mukuyendamo. Bwerera, iwe namwali wa Israeli, bwerera ku mizinda yako ija.
הציבי לך צינים שמי לך תמרורים--שתי לבך למסלה דרך הלכתי (הלכת) שובי בתולת ישראל שבי אל עריך אלה
22 Udzakhala jenkha mpaka liti, iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika? Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
עד מתי תתחמקין הבת השובבה כי ברא יהוה חדשה בארץ נקבה תסובב גבר
23 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’
כה אמר יהוה צבאות אלהי ישראל עוד יאמרו את הדבר הזה בארץ יהודה ובעריו בשובי את שבותם יברכך יהוה נוה צדק הר הקדש
24 Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa.
וישבו בה יהודה וכל עריו יחדו אכרים ונסעו בעדר
25 Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”
כי הרויתי נפש עיפה וכל נפש דאבה מלאתי
26 Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.
על זאת הקיצתי ואראה ושנתי ערבה לי
27 “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda.
הנה ימים באים נאם יהוה וזרעתי את בית ישראל ואת בית יהודה זרע אדם וזרע בהמה
28 Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova.
והיה כאשר שקדתי עליהם לנתוש ולנתוץ ולהרס--ולהאביד ולהרע כן אשקד עליהם לבנות ולנטוע נאם יהוה
29 “Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti, “Makolo adya mphesa zosapsa, koma mano a ana ndiye achita dziru.
בימים ההם--לא יאמרו עוד אבות אכלו בסר ושני בנים תקהינה
30 Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”
כי אם איש בעונו ימות כל האדם האכל הבסר תקהינה שניו
31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachita pangano latsopano ndi Aisraeli ndiponso nyumba ya Yuda.
הנה ימים באים נאם יהוה וכרתי את בית ישראל ואת בית יהודה--ברית חדשה
32 Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto; chifukwa anaphwanya pangano langa, ngakhale ndinali mwamuna wawo,” akutero Yehova.
לא כברית אשר כרתי את אבותם ביום החזיקי בידם להוציאם מארץ מצרים אשר המה הפרו את בריתי ואנכי בעלתי בם--נאם יהוה
33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.
כי זאת הברית אשר אכרת את בית ישראל אחרי הימים ההם נאם יהוה נתתי את תורתי בקרבם ועל לבם אכתבנה והייתי להם לאלהים והמה יהיו לי לעם
34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake, kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’ chifukwa onse adzandidziwa Ine, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,” akutero Yehova. “Ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
ולא ילמדו עוד איש את רעהו ואיש את אחיו לאמר דעו את יהוה כי כולם ידעו אותי למקטנם ועד גדולם נאם יהוה--כי אסלח לעונם ולחטאתם לא אזכר עוד
35 Yehova akuti, Iye amene amakhazikitsa dzuwa kuti liziwala masana, amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi ziziwala usiku, amene amavundula nyanja kuti mafunde akokome, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
כה אמר יהוה נתן שמש לאור יומם חקת ירח וכוכבים לאור לילה רגע הים ויהמו גליו יהוה צבאות שמו
36 Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.
אם ימשו החקים האלה מלפני--נאם יהוה גם זרע ישראל ישבתו מהיות גוי לפני--כל הימים
37 Yehova akuti, “Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo. Ngati patapezeka munthu amene angathe kupima zakuthambo nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”
כה אמר יהוה אם ימדו שמים מלמעלה ויחקרו מוסדי ארץ למטה גם אני אמאס בכל זרע ישראל על כל אשר עשו--נאם יהוה
38 “Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya.
הנה ימים (באים) נאם יהוה ונבנתה העיר ליהוה ממגדל חננאל שער הפנה
39 Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa.
ויצא עוד קוה (קו) המדה נגדו על גבעת גרב ונסב געתה
40 Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”
וכל העמק הפגרים והדשן וכל השרמות (השדמות) עד נחל קדרון עד פנת שער הסוסים מזרחה--קדש ליהוה לא ינתש ולא יהרס עוד לעולם

< Yeremiya 31 >