< Yeremiya 30 >

1 Yehova anawuza Yeremiya kuti,
הדבר אשר היה אל ירמיהו מאת יהוה לאמר
2 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza.
כה אמר יהוה אלהי ישראל לאמר כתב לך את כל הדברים אשר דברתי אליך--אל ספר
3 Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
כי הנה ימים באים נאם יהוה ושבתי את שבות עמי ישראל ויהודה אמר יהוה והשבתים אל הארץ אשר נתתי לאבותם--וירשוה
4 Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda:
ואלה הדברים אשר דבר יהוה אל ישראל--ואל יהודה
5 “Yehova akuti: “Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa, ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
כי כה אמר יהוה קול חרדה שמענו--פחד ואין שלום
6 Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti: Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
שאלו נא וראו אם ילד זכר מדוע ראיתי כל גבר ידיו על חלציו כיולדה ונהפכו כל פנים לירקון
7 Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri! Sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo, koma adzapulumuka ku masautsowo.”
הוי כי גדול היום ההוא--מאין כמהו ועת צרה היא ליעקב וממנה יושע
8 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo ndipo ndidzadula zingwe zowamanga; Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
והיה ביום ההוא נאם יהוה צבאות אשבר עלו מעל צוארך ומוסרותיך אנתק ולא יעבדו בו עוד זרים
9 Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo ndiponso Davide mfumu yawo, amene ndidzawasankhira.
ועבדו את יהוה אלהיהם ואת דוד מלכם אשר אקים להם
10 “‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo; usade nkhawa, iwe Israeli,’ akutero Yehova. ‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali, zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo. Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere, ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
ואתה אל תירא עבדי יעקב נאם יהוה ואל תחת ישראל--כי הנני מושיעך מרחוק ואת זרעך מארץ שבים ושב יעקב ושקט ושאנן ואין מחריד
11 Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu kumene ndinakubalalitsirani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa. Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’”
כי אתך אני נאם יהוה להושיעך כי אעשה כלה בכל הגוים אשר הפצותיך שם אך אתך לא אעשה כלה ויסרתיך למשפט ונקה לא אנקך
12 Yehova akuti, “Chilonda chanu nʼchosachizika, bala lanu ndi lonyeka.
כי כה אמר יהוה אנוש לשברך--נחלה מכתך
13 Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu, palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira, palibe mankhwala ochiritsa inu.
אין דן דינך למזור רפאות תעלה אין לך
14 Abwenzi anu onse akuyiwalani; sasamalanso za inu. Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira. Ndipo ndakulangani mwa nkhanza, chifukwa machimo anu ndi ambiri, ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
כל מאהביך שכחוך אותך לא ידרשו כי מכת אויב הכיתיך מוסר אכזרי--על רב עונך עצמו חטאתיך
15 Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ayi. Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
מה תזעק על שברך אנוש מכאבך על רב עונך עצמו חטאתיך--עשיתי אלה לך
16 “Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa; adani anu onse adzapita ku ukapolo. Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso; onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
לכן כל אכליך יאכלו וכל צריך כלם בשבי ילכו והיו שאסיך למשסה וכל בזזיך אתן לבז
17 Ndidzachiza matenda anu ndi kupoletsa zilonda zanu, akutero Yehova, ‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika. Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’”
כי אעלה ארכה לך וממכותיך ארפאך נאם יהוה כי נדחה קראו לך--ציון היא דרש אין לה
18 Yehova akuti, “Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo; mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake, nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
כה אמר יהוה הנני שב שבות אהלי יעקוב ומשכנתיו ארחם ונבנתה עיר על תלה וארמון על משפטו ישב
19 Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo. Ndidzawachulukitsa, ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika; ndidzawapatsa ulemerero, ndipo sadzanyozedwanso.
ויצא מהם תודה וקול משחקים והרבתים ולא ימעטו והכבדתים ולא יצערו
20 Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale, ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga; ndidzalanga onse owazunza.
והיו בניו כקדם ועדתו לפני תכון ופקדתי על כל לחציו
21 Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo. Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo. Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira. Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane popanda kuyitanidwa?” akutero Yehova.
והיה אדירו ממנו ומשלו מקרבו יצא והקרבתיו ונגש אלי כי מי הוא זה ערב את לבו לגשת אלי--נאם יהוה
22 “Choncho inu mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”
והייתם לי לעם ואנכי אהיה לכם לאלהים
23 Taonani ukali wa Yehova wowomba ngati mphepo ya mkuntho. Mphepo ya namondwe ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
הנה סערת יהוה חמה יצאה--סער מתגורר על ראש רשעים יחול
24 Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka mpaka atakwaniritsa zolinga za mu mtima mwake. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.
לא ישוב חרון אף יהוה עד עשתו ועד הקימו מזמות לבו באחרית הימים תתבוננו בה

< Yeremiya 30 >