< Yesaya 25 >

1 Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri.
O LORD, You are my God! I will exalt You; I will praise Your name. For You have worked wonders— plans formed long ago— in perfect faithfulness.
2 Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala. Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja, linga la anthu achilendo lero si mzindanso ndipo sidzamangidwanso.
Indeed, You have made the city a heap of rubble, the fortified town a ruin. The fortress of strangers is a city no more; it will never be rebuilt.
3 Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani; mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
Therefore, a strong people will honor You. The cities of ruthless nations will revere You.
4 Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka, mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake. Mwakhala ngati pobisalirapo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa. Pakuti anthu ankhanza ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
For You have been a refuge for the poor, a stronghold for the needy in distress, a refuge from the storm, a shade from the heat. For the breath of the ruthless is like rain against a wall,
5 ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha, inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
like heat in a dry land. You subdue the uproar of foreigners. As the shade of a cloud cools the heat, so the song of the ruthless is silenced.
6 Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino. Phwando la nyama yonona ndi vinyo wabwino kwambiri.
On this mountain the LORD of Hosts will prepare a banquet for all the peoples, a feast of aged wine, of choice meat, of finely aged wine.
7 Iye adzachotsa kulira kumene kwaphimba anthu ngati nsalu. Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
On this mountain He will swallow up the shroud that enfolds all peoples, the sheet that covers all nations;
8 Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.
He will swallow up death forever. The Lord GOD will wipe away the tears from every face and remove the disgrace of His people from the whole earth.
9 Tsiku limenelo iwo adzati, “Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu; ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira; tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
And in that day it will be said, “Surely this is our God; we have waited for Him, and He has saved us. This is the LORD for whom we have waited. Let us rejoice and be glad in His salvation.”
10 Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake; ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo, ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
For the hand of the LORD will rest on this mountain. But Moab will be trampled in his place as straw is trodden into the dung pile.
11 Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo, ngati mmene amachitira munthu wosambira. Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo ngakhale luso la manja awo.
He will spread out his hands within it, as a swimmer spreads his arms to swim. His pride will be brought low, despite the skill of his hands.
12 Iye adzagumula malinga awo ataliatali ndipo adzawagwetsa ndi kuwaponya pansi, pa fumbi penipeni.
The high-walled fortress will be brought down, cast to the ground, into the dust.

< Yesaya 25 >