Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Isaiah Chapter 25 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Isaiah/25 1) Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri. 2) Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala. Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja, linga la anthu achilendo lero si mzindanso ndipo sidzamangidwanso. 3) Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani; mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani. 4) Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka, mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake. Mwakhala ngati pobisalirapo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa. Pakuti anthu ankhanza ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma, 5) ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha, inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza. 6) Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino. Phwando la nyama yonona ndi vinyo wabwino kwambiri. 7) Iye adzachotsa kulira kumene kwaphimba anthu ngati nsalu. Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu. 8) Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula. 9) Tsiku limenelo iwo adzati, “Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu; ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira; tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.” 10) Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake; ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo, ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje. 11) Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo, ngati mmene amachitira munthu wosambira. Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo ngakhale luso la manja awo. 12) Iye adzagumula malinga awo ataliatali ndipo adzawagwetsa ndi kuwaponya pansi, pa fumbi penipeni. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!