< Ezekieli 18 >

1 Yehova anandiyankhula nati:
וַיְהִ֥י דְבַר־יְהוָ֖ה אֵלַ֥י לֵאמֹֽר׃
2 “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti: “‘Nkhuyu zodya akulu zimapota ndi ana omwe?’”
מַה־לָּכֶ֗ם אַתֶּם֙ מֹֽשְׁלִים֙ אֶת־הַמָּשָׁ֣ל הַזֶּ֔ה עַל־אַדְמַ֥ת יִשְׂרָאֵ֖ל לֵאמֹ֑ר אָבֹות֙ יֹ֣אכְלוּ בֹ֔סֶר וְשִׁנֵּ֥י הַבָּנִ֖ים תִּקְהֶֽינָה׃
3 “Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli.
חַי־אָ֕נִי נְאֻ֖ם אֲדֹנָ֣י יְהוִ֑ה אִם־יִֽהְיֶ֨ה לָכֶ֜ם עֹ֗וד מְשֹׁ֛ל הַמָּשָׁ֥ל הַזֶּ֖ה בְּיִשְׂרָאֵֽל׃
4 Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.
הֵ֤ן כָּל־הַנְּפָשֹׁות֙ לִ֣י הֵ֔נָּה כְּנֶ֧פֶשׁ הָאָ֛ב וּכְנֶ֥פֶשׁ הַבֵּ֖ן לִי־הֵ֑נָּה הַנֶּ֥פֶשׁ הַחֹטֵ֖את הִ֥יא תָמֽוּת׃ ס
5 “Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama amene amachita zolungama ndi zolondola.
וְאִ֖ישׁ כִּי־יִהְיֶ֣ה צַדִּ֑יק וְעָשָׂ֥ה מִשְׁפָּ֖ט וּצְדָקָֽה׃
6 Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo kapena kupembedza mafano a Aisraeli. Iye sayipitsa mkazi wa mnzake kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
אֶל־הֶֽהָרִים֙ לֹ֣א אָכָ֔ל וְעֵינָיו֙ לֹ֣א נָשָׂ֔א אֶל־גִּלּוּלֵ֖י בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֑ל וְאֶת־אֵ֤שֶׁת רֵעֵ֙הוּ֙ לֹ֣א טִמֵּ֔א וְאֶל־אִשָּׁ֥ה נִדָּ֖ה לֹ֥א יִקְרָֽב׃
7 Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
וְאִישׁ֙ לֹ֣א יֹונֶ֔ה חֲבֹלָתֹ֥ו חֹוב֙ יָשִׁ֔יב גְּזֵלָ֖ה לֹ֣א יִגְזֹ֑ל לַחְמֹו֙ לְרָעֵ֣ב יִתֵּ֔ן וְעֵירֹ֖ם יְכַסֶּה־בָּֽגֶד׃
8 Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira, kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu. Amadziletsa kuchita zoyipa ndipo sakondera poweruza milandu.
בַּנֶּ֣שֶׁךְ לֹֽא־יִתֵּ֗ן וְתַרְבִּית֙ לֹ֣א יִקָּ֔ח מֵעָ֖וֶל יָשִׁ֣יב יָדֹ֑ו מִשְׁפַּ֤ט אֱמֶת֙ יַֽעֲשֶׂ֔ה בֵּ֥ין אִ֖ישׁ לְאִֽישׁ׃
9 Iye amatsatira malangizo anga, ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika. Munthu ameneyo ndi wolungama; iye adzakhala ndithu ndi moyo, akutero Ambuye Yehova.
בְּחֻקֹּותַ֧י יְהַלֵּ֛ךְ וּמִשְׁפָּטַ֥י שָׁמַ֖ר לַעֲשֹׂ֣ות אֱמֶ֑ת צַדִּ֥יק הוּא֙ חָיֹ֣ה יִֽחְיֶ֔ה נְאֻ֖ם אֲדֹנָ֥י יְהוִֽה׃
10 “Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere.
וְהֹולִ֥יד בֵּן־פָּרִ֖יץ שֹׁפֵ֣ךְ דָּ֑ם וְעָ֣שָׂה אָ֔ח מֵאַחַ֖ד מֵאֵֽלֶּה׃
11 Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo. “Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo. Amayipitsa mkazi wa mnzake.
וְה֕וּא אֶת־כָּל־אֵ֖לֶּה לֹ֣א עָשָׂ֑ה כִּ֣י גַ֤ם אֶל־הֶֽהָרִים֙ אָכַ֔ל וְאֶת־אֵ֥שֶׁת רֵעֵ֖הוּ טִמֵּֽא׃
12 Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa. Amalanda zinthu za osauka. Sabweza chikole cha munthu wa ngongole. Iye amatembenukira ku mafano nachita zonyansa.
עָנִ֤י וְאֶבְיֹון֙ הֹונָ֔ה גְּזֵלֹ֣ות גָּזָ֔ל חֲבֹ֖ל לֹ֣א יָשִׁ֑יב וְאֶל־הַגִּלּוּלִים֙ נָשָׂ֣א עֵינָ֔יו תֹּועֵבָ֖ה עָשָֽׂה׃
13 Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu. Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.
בַּנֶּ֧שֶׁךְ נָתַ֛ן וְתַרְבִּ֥ית לָקַ֖ח וָחָ֑י לֹ֣א יִֽחְיֶ֗ה אֵ֣ת כָּל־הַתֹּועֵבֹ֤ות הָאֵ֙לֶּה֙ עָשָׂ֔ה מֹ֣ות יוּמָ֔ת דָּמָ֖יו בֹּ֥ו יִהְיֶֽה׃
14 “Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.
וְהִנֵּה֙ הֹולִ֣יד בֵּ֔ן וַיַּ֕רְא אֶת־כָּל־חַטֹּ֥את אָבִ֖יו אֲשֶׁ֣ר עָשָׂ֑ה וַיִּרְאֶ֕ה וְלֹ֥א יַעֲשֶׂ֖ה כָּהֵֽן׃
15 “Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israeli. Sayipitsa mkazi wa mnzake.
עַל־הֶֽהָרִים֙ לֹ֣א אָכָ֔ל וְעֵינָיו֙ לֹ֣א נָשָׂ֔א אֶל־גִּלּוּלֵ֖י בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֑ל אֶת־אֵ֥שֶׁת רֵעֵ֖הוּ לֹ֥א טִמֵּֽא׃
16 Sapondereza munthu wina aliyense. Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka. Salanda zinthu za munthu. Amapereka chakudya kwa anthu anjala. Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
וְאִישׁ֙ לֹ֣א הֹונָ֔ה חֲבֹל֙ לֹ֣א חָבָ֔ל וּגְזֵלָ֖ה לֹ֣א גָזָ֑ל לַחְמֹו֙ לְרָעֵ֣ב נָתָ֔ן וְעֵרֹ֖ום כִּסָּה־בָֽגֶד׃
17 Amadziletsa kuchita zoyipa. Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja. Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu.
מֵעָנִ֞י הֵשִׁ֣יב יָדֹ֗ו נֶ֤שֶׁךְ וְתַרְבִּית֙ לֹ֣א לָקָ֔ח מִשְׁפָּטַ֣י עָשָׂ֔ה בְּחֻקֹּותַ֖י הָלָ֑ךְ ה֗וּא לֹ֥א יָמ֛וּת בַּעֲוֹ֥ן אָבִ֖יו חָיֹ֥ה יִחְיֶֽה׃
18 Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.
אָבִ֞יו כִּֽי־עָ֣שַׁק עֹ֗שֶׁק גָּזַל֙ גֵּ֣זֶל אָ֔ח וַאֲשֶׁ֥ר לֹא־טֹ֛וב עָשָׂ֖ה בְּתֹ֣וךְ עַמָּ֑יו וְהִנֵּה־מֵ֖ת בַּעֲוֹנֹֽו׃
19 “Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse.
וַאֲמַרְתֶּ֕ם מַדֻּ֛עַ לֹא־נָשָׂ֥א הַבֵּ֖ן בַּעֲוֹ֣ן הָאָ֑ב וְהַבֵּ֞ן מִשְׁפָּ֧ט וּצְדָקָ֣ה עָשָׂ֗ה אֵ֣ת כָּל־חֻקֹּותַ֥י שָׁמַ֛ר וַיַּעֲשֶׂ֥ה אֹתָ֖ם חָיֹ֥ה יִחְיֶֽה׃
20 Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.
הַנֶּ֥פֶשׁ הַחֹטֵ֖את הִ֣יא תָמ֑וּת בֵּ֞ן לֹא־יִשָּׂ֣א ׀ בַּעֲוֹ֣ן הָאָ֗ב וְאָב֙ לֹ֤א יִשָּׂא֙ בַּעֲוֹ֣ן הַבֵּ֔ן צִדְקַ֤ת הַצַּדִּיק֙ עָלָ֣יו תִּֽהְיֶ֔ה וְרִשְׁעַ֥ת רָשָׁע (הָרָשָׁ֖ע) עָלָ֥יו תִּֽהְיֶֽה׃ ס
21 “‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi.
וְהָרָשָׁ֗ע כִּ֤י יָשׁוּב֙ מִכָּל־חַטָּאתֹו (חַטֹּאתָיו֙) אֲשֶׁ֣ר עָשָׂ֔ה וְשָׁמַר֙ אֶת־כָּל־חֻקֹותַ֔י וְעָשָׂ֥ה מִשְׁפָּ֖ט וּצְדָקָ֑ה חָיֹ֥ה יִחְיֶ֖ה לֹ֥א יָמֽוּת׃
22 Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo.
כָּל־פְּשָׁעָיו֙ אֲשֶׁ֣ר עָשָׂ֔ה לֹ֥א יִזָּכְר֖וּ לֹ֑ו בְּצִדְקָתֹ֥ו אֲשֶׁר־עָשָׂ֖ה יִֽחְיֶֽה׃
23 Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.
הֶחָפֹ֤ץ אֶחְפֹּץ֙ מֹ֣ות רָשָׁ֔ע נְאֻ֖ם אֲדֹנָ֣י יְהוִ֑ה הֲלֹ֛וא בְּשׁוּבֹ֥ו מִדְּרָכָ֖יו וְחָיָֽה׃ ס
24 “‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.
וּבְשׁ֨וּב צַדִּ֤יק מִצִּדְקָתֹו֙ וְעָ֣שָׂה עָ֔וֶל כְּכֹ֨ל הַתֹּועֵבֹ֜ות אֲשֶׁר־עָשָׂ֧ה הָרָשָׁ֛ע יַעֲשֶׂ֖ה וָחָ֑י כָּל־צִדְקָתֹו (צִדְקֹתָ֤יו) אֲשֶׁר־עָשָׂה֙ לֹ֣א תִזָּכַ֔רְנָה בְּמַעֲלֹ֧ו אֲשֶׁר־מָעַ֛ל וּבְחַטָּאתֹ֥ו אֲשֶׁר־חָטָ֖א בָּ֥ם יָמֽוּת׃
25 “Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama?
וַאֲמַרְתֶּ֕ם לֹ֥א יִתָּכֵ֖ן דֶּ֣רֶךְ אֲדֹנָ֑י שִׁמְעוּ־נָא֙ בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֔ל הֲדַרְכִּי֙ לֹ֣א יִתָּכֵ֔ן הֲלֹ֥א דַרְכֵיכֶ֖ם לֹ֥א יִתָּכֵֽנוּ׃
26 Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo.
בְּשׁוּב־צַדִּ֧יק מִצִּדְקָתֹ֛ו וְעָ֥שָׂה עָ֖וֶל וּמֵ֣ת עֲלֵיהֶ֑ם בְּעַוְלֹ֥ו אֲשֶׁר־עָשָׂ֖ה יָמֽוּת׃ ס
27 Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake.
וּבְשׁ֣וּב רָשָׁ֗ע מֵֽרִשְׁעָתֹו֙ אֲשֶׁ֣ר עָשָׂ֔ה וַיַּ֥עַשׂ מִשְׁפָּ֖ט וּצְדָקָ֑ה ה֖וּא אֶת־נַפְשֹׁ֥ו יְחַיֶּֽה׃
28 Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa.
וַיִּרְאֶ֣ה וַיָּשֹׁוב (וַיָּ֔שָׁב) מִכָּל־פְּשָׁעָ֖יו אֲשֶׁ֣ר עָשָׂ֑ה חָיֹ֥ו יִחְיֶ֖ה לֹ֥א יָמֽוּת׃
29 Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?
וְאָֽמְרוּ֙ בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֔ל לֹ֥א יִתָּכֵ֖ן דֶּ֣רֶךְ אֲדֹנָ֑י הַדְּרָכַ֞י לֹ֤א יִתָּֽכְנּוּ֙ בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֔ל הֲלֹ֥א דַרְכֵיכֶ֖ם לֹ֥א יִתָּכֵֽן׃
30 “Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo.
לָכֵן֩ אִ֨ישׁ כִּדְרָכָ֜יו אֶשְׁפֹּ֤ט אֶתְכֶם֙ בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֔ל נְאֻ֖ם אֲדֹנָ֣י יְהוִ֑ה שׁ֤וּבוּ וְהָשִׁ֙יבוּ֙ מִכָּל־פִּשְׁעֵיכֶ֔ם וְלֹֽא־יִהְיֶ֥ה לָכֶ֛ם לְמִכְשֹׁ֖ול עָוֹֽן׃
31 Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli?
הַשְׁלִ֣יכוּ מֵעֲלֵיכֶ֗ם אֶת־כָּל־פִּשְׁעֵיכֶם֙ אֲשֶׁ֣ר פְּשַׁעְתֶּ֣ם בָּ֔ם וַעֲשׂ֥וּ לָכֶ֛ם לֵ֥ב חָדָ֖שׁ וְר֣וּחַ חֲדָשָׁ֑ה וְלָ֥מָּה תָמֻ֖תוּ בֵּ֥ית יִשְׂרָאֵֽל׃
32 Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”
כִּ֣י לֹ֤א אֶחְפֹּץ֙ בְּמֹ֣ות הַמֵּ֔ת נְאֻ֖ם אֲדֹנָ֣י יְהוִ֑ה וְהָשִׁ֖יבוּ וִֽחְיֽוּ׃ פ

< Ezekieli 18 >