Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Ezekiel Chapter 18 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Ezekiel/18 1) Yehova anandiyankhula nati: 2) “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti: “‘Nkhuyu zodya akulu zimapota ndi ana omwe?’” 3) “Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. 4) Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe. 5) “Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama amene amachita zolungama ndi zolondola. 6) Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo kapena kupembedza mafano a Aisraeli. Iye sayipitsa mkazi wa mnzake kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba. 7) Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa. 8) Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira, kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu. Amadziletsa kuchita zoyipa ndipo sakondera poweruza milandu. 9) Iye amatsatira malangizo anga, ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika. Munthu ameneyo ndi wolungama; iye adzakhala ndithu ndi moyo, akutero Ambuye Yehova. 10) “Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. 11) Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo. “Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo. Amayipitsa mkazi wa mnzake. 12) Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa. Amalanda zinthu za osauka. Sabweza chikole cha munthu wa ngongole. Iye amatembenukira ku mafano nachita zonyansa. 13) Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu. Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera. 14) “Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo. 15) “Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israeli. Sayipitsa mkazi wa mnzake. 16) Sapondereza munthu wina aliyense. Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka. Salanda zinthu za munthu. Amapereka chakudya kwa anthu anjala. Amapereka zovala kwa anthu aumphawi. 17) Amadziletsa kuchita zoyipa. Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja. Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. 18) Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe. 19) “Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. 20) Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse. 21) “‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 22) Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. 23) Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova. 24) “‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita. 25) “Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? 26) Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. 27) Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. 28) Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. 29) Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo? 30) “Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. 31) Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? 32) Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.” Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!