< 2 Mbiri 9 >
1 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
La reina de Saba se enteró de la fama de Salomón y vino a Jerusalén para ponerle a prueba con preguntas difíciles. Trajo consigo un séquito muy numeroso, con camellos cargados de especias, grandes cantidades de oro y piedras preciosas. Se acercó a Salomón y le preguntó todo lo que tenía en mente.
2 Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta kwa iye komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo.
Salomón respondió a todas sus preguntas. No había nada que no pudiera explicarle.
3 Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru za Solomoni komanso nyumba yaufumu imene anamanga,
Cuando la reina de Saba vio la sabiduría de Salomón y el palacio que había construido,
4 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo; atumiki opereka zakumwa ndi zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
la comida que había en la mesa, cómo vivían sus funcionarios, cómo funcionaban sus sirvientes y cómo estaban vestidos, las ropas de los camareros y los holocaustos que presentaba en el Templo del Señor, quedó tan asombrada que apenas podía respirar.
5 Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu, ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona.
Le dijo al rey: “Es cierto lo que he oído en mi país sobre tus proverbios ¡y tu sabiduría!
6 Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva.
Pero no creí lo que me dijeron hasta que vine y lo vi con mis propios ojos. De hecho, no me contaron ni la mitad: ¡la extensión de tu sabiduría supera con creces lo que he oído!
7 Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu!
¡Qué feliz debe ser tu pueblo! ¡Qué felices los que trabajan para ti, los que están aquí cada día escuchando tu sabiduría!
8 Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
Alabado sea el Señor, tu Dios, que tanto se complace en ti, que te puso en su trono como rey para gobernar en su nombre. Por el amor de tu Dios a Israel los ha asegurado para siempre, y te ha hecho rey sobre ellos para que hagas lo justo y lo correcto”.
9 Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni.
Presentó al rey ciento veinte talentos de oro, enormes cantidades de especias y piedras preciosas. Nunca antes había habido especias como las que la reina de Saba regaló al rey Salomón.
10 (Anthu a Hiramu ndi anthu a Solomoni anabweretsa golide kuchokera ku Ofiri ndipo anabweretsanso mitengo ya mʼbawa ndi miyala yokongola.
(Hiram y los hombres de Salomón, que trajeron oro de Ofir, también trajeron madera de algum y piedras preciosas.
11 Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya mʼbawa pokonzera makwerero a Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndiponso kupangira anthu oyimba apangwe ndi azeze. Zinthu zonga zimenezi sizinaonekeponso mu Yuda).
El rey utilizó la madera de algum para hacer escalones para el Templo y para el palacio real, y en liras y arpas para los músicos. Nunca se había visto nada igual en el país de Judá).
12 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake.
El rey Salomón dio a la reina de Saba todo lo que quiso, todo lo que pidió. Esto era mucho más de lo que ella había traído al rey. Luego, ella y sus acompañantes regresaron a su país.
13 Kulemera kwa golide amene Solomoni amalandira pa chaka kunali makilogalamu 23,000,
El peso del oro que Salomón recibía cada año era de 666 talentos,
14 osawerengera amene ankabwera ndi anthu ochita malonda ndi osinthanitsa zinthu. Komanso mafumu onse a ku Arabiya ndi abwanamkubwa a mʼdzikomo amabweretsa golide ndi siliva kwa Solomoni.
sin incluir el que recibía de los comerciantes y mercaderes. Todos los reyes de Arabia y los gobernadores del país también le llevaban oro y plata a Salomón.
15 Mfumu Solomoni inapanga zishango zazikulu 200 zagolide wosasantha. Mʼchishango chilichonse mumalowa golide wolemera makilogalamu asanu ndi awiri.
El rey Salomón hizo doscientos escudos de oro martillado. Cada escudo requería seiscientos siclos de oro martillado.
16 Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
También hizo trescientos escudos pequeños de oro martillado. Cada uno de estos escudos requería trescientas monedas de oro. El rey los colocó en el Palacio del Bosque del Líbano.
17 Ndipo mfumu inapanganso mpando waukulu waufumu wa nyanga za njovu ndipo unakutidwa ndi golide woyengeka bwino.
El rey hizo también un gran trono de marfil y lo cubrió de oro puro.
18 Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi ndi choyikapo mapazi cholumikizidwa ku mpandowo. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, ndi chifanizo cha mkango chitayima posanjikapo manjapo.
El trono tenía seis escalones, con un escabel de oro adosado. A ambos lados del asiento había reposabrazos, con leones de pie junto a los reposabrazos.
19 Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi imodzi aja. Umodzi mbali ina ya khwerero ndi wina mbali inayo. Palibe mpando wonga uwu umene unapangidwapo mu ufumu wina uliwonse.
En los seis escalones había doce leones, uno en cada extremo de cada escalón. Nunca se había hecho nada parecido para ningún reino.
20 Zikho zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndiponso zipangizo zonse za ku nyumba yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide oyengeka bwino. Panalibe chinthu chopangidwa ndi siliva, chifukwa siliva samayesedwa kanthu mʼnthawi ya Solomoni.
Todas las copas del rey Salomón eran de oro, y todos los utensilios del Palacio del Bosque del Líbano eran de oro puro. No se usó plata, porque no era valorada en los días de Salomón.
21 Mfumu inali ndi sitima zambiri zapamadzi zimene zimayendetsedwa ndi antchito a Hiramu. Zimabwera kamodzi pa zaka zitatu zilizonse zitanyamula golide, siliva ndi nyanga za njovu, ndiponso anyani ndi apusi.
El rey tenía una flota de barcos de Tarsis tripulada por marineros de Hiram. Una vez cada tres años los barcos de Tarsis llegaban con un cargamento de oro, plata, marfil, monos y pavos reales.
22 Mfumu Solomoni anapambana mafumu ena onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru.
El rey Salomón era más grande que cualquier otro rey de la tierra en riqueza y sabiduría.
23 Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake.
Todos los reyes de la tierra querían conocer a Salomón para escuchar la sabiduría que Dios había puesto en su mente.
24 Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu.
Año tras año, todos los visitantes traían regalos: objetos de plata y oro, ropa, armas, especias, caballos y mulas.
25 Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo ndi magaleta, ndi akavalo 12,000 amene amawasunga mʼmizinda yosungira magaleta ndiponso ena anali ndi iye ku Yerusalemu.
Salomón tenía cuatro mil establos para caballos y carros, y doce mil jinetes. Los mantuvo en las ciudades de los carros, y también con él en Jerusalén.
26 Iye ankalamulira mafumu onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika ku malire a dziko la Igupto.
Dominó a todos los reyes desde el río Éufrates hasta el país de los filisteos y hasta la frontera con Egipto.
27 Mfumu inasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba mu Yerusalemu ndipo mikungudza kukhala yochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa.
El rey hizo que en Jerusalén abundara la plata como las piedras, y la madera de cedro como los sicómoros en las estribaciones.
28 Solomoni ankayitanitsa akavalo ake kuchokera ku Igupto ndi mayiko ena onse.
Los caballos de Salomón fueron importados de Egipto y de muchas otras tierras.
29 Tsono ntchito zina zonse za Solomoni, kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza, kodi sizinalembedwa mʼbuku la mbiri la mneneri Natani, ndi mʼbuku la uneneri wa Ahiya wa ku Silo ndi mʼbuku la masomphenya a mlosi Ido, lokamba za Yeroboamu mwana wa Nebati?
El resto de los hechos de Salomón, desde el principio hasta el final, están escritos en las Actas de Natán el Profeta, en la Profecía de Ahías el Silonita y en las Visiones de Iddo el Vidente acerca Jeroboam, hijo de Nabat.
30 Solomoni analamulira Aisraeli onse ku Yerusalemu zaka makumi anayi.
Salomón gobernó en Jerusalén sobre todo Israel durante cuarenta años.
31 Ndipo anamwalira nagona ndi makolo ake. Anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
Luego Salomón murió y fue enterrado en la ciudad de su padre David. Su hijo Roboam asumió como rey.