< 1 Akorinto 4 >
1 Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu.
Let a man so account of us, as of ministers of Christ, and stewards of the mysteries of God.
2 Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika.
Here, moreover, it is required in stewards, that a man be found faithful.
3 Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha.
But with me it is a very small thing that I should be judged of you, or of man’s judgment: yea, I judge not mine own self.
4 Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye.
For I know nothing against myself; yet am I not hereby justified: but he that judgeth me is the Lord.
5 Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.
Wherefore judge nothing before the time, until the Lord come, who will both bring to light the hidden things of darkness, and make manifest the counsels of the hearts; and then shall each man have his praise from God.
6 Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake.
Now these things, brethren, I have in a figure transferred to myself and Apollos for your sakes; that in us ye might learn not [to go] beyond the things which are written; that no one of you be puffed up for the one against the other.
7 Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire?
For who maketh thee to differ? and what hast thou that thou didst not receive? but if thou didst receive it, why dost thou glory, as if thou hadst not received it?
8 Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu.
Already are ye filled, already ye are become rich, ye have reigned without us: yea and I would that ye did reign, that we also might reign with you.
9 Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu.
For, I think, God hath set forth us the apostles last of all, as men doomed to death: for we are made a spectacle unto the world, and to angels, and to men.
10 Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa!
We are fools for Christ’s sake, but ye are wise in Christ; we are weak, but ye are strong; ye have glory, but we have dishonour.
11 Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba.
Even unto this present hour we both hunger, and thirst, and are naked, and are buffeted, and have no certain dwelling place;
12 Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira.
and we toil, working with our own hands: being reviled, we bless; being persecuted, we endure;
13 Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.
being defamed, we entreat: we are made as the filth of the world, the offscouring of all things, even until now.
14 Sindikulemba izi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kukuchenjezani monga ana anga okondedwa.
I write not these things to shame you, but to admonish you as my beloved children.
15 Ngakhale muli ndi anthu 10,000 okutsogolerani mwa Khristu, mulibe abambo ambiri, popeza mwa Khristu Yesu, ine ndakhala abambo anu kudzera mu Uthenga Wabwino.
For though ye should have ten thousand tutors in Christ, yet [have ye] not many fathers: for in Christ Jesus I begat you through the gospel.
16 Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine.
I beseech you therefore, be ye imitators of me.
17 Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo, mwana wanga amene ndimamukonda, amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu, umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse.
For this cause have I sent unto you Timothy, who is my beloved and faithful child in the Lord, who shall put you in remembrance of my ways which be in Christ, even as I teach everywhere in every church.
18 Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu.
Now some are puffed up, as though I were not coming to you.
19 Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani.
But I will come to you shortly, if the Lord will; and I will know, not the word of them which are puffed up, but the power.
20 Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu.
For the kingdom of God is not in word, but in power.
21 Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?
What will ye? shall I come unto you with a rod, or in love and a spirit of meekness?