Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Song-of-Solomon Chapter 3 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Song-of-Solomon/3 1) Usiku wonse ndili pa bedi langa ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda; ndinamufunafuna koma osamupeza. 2) Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda, mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake; ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda. Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza. 3) Alonda anandipeza pamene ankayendera mzinda. “Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?” 4) Nditawapitirira pangʼono ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda. Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, mʼchipinda cha amene anandibereka. 5) Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. 6) Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu ngati utsi watolotolo, wonunkhira mure ndi lubani, zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda? 7) Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni, choperekezedwa ndi asilikali 60, anthu amphamvu a ku Israeli, 8) onse atanyamula lupanga, onse odziwa bwino nkhondo, aliyense ali ndi lupanga pambali pake, kukonzekera zoopsa za usiku. 9) Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi; anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni. 10) Milongoti yake anayipanga yasiliva, kumbuyo kwake kwa golide. Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo, anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi cha akazi a ku Yerusalemu. 11) Tukulani inu akazi a ku Ziyoni ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu, chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unasangalala. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!