Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Romans Chapter 7 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Romans/7 1) Kodi simukudziwa abale kuti Malamulo ali ndi ulamuliro pa munthu pokhapokha ngati ali ndi moyo? Ine ndikuyankhula kwa anthu amene akudziwa Malamulo. 2) Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati. 3) Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina. 4) Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso. 5) Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa. 6) Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa. 7) Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.” 8) Koma chifukwa cha Malamulo uchimo unapeza mwayi owutsa mʼkati mwanga khalidwe lililonse la kusirira. Pakuti pakanapanda Malamulo, uchimo ukanakhala wopanda mphamvu. 9) Nthawi ina ndinali ndi moyo popanda Malamulo. Koma nditayamba kudziwa Malamulo, pomwepo uchimo unayamba kuphuka, 10) ndipo ine ndinafa. Ine ndinazindikira kuti Malamulo omwe ankayenera kubweretsa moyo anabweretsa imfa. 11) Pakuti uchimo unapeza mwayi chifukwa cha Malamulo ndipo kudzera mʼMalamulowo, unandinyenga ndi kundiyika mu imfa. 12) Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino. 13) Kodi chomwe ndi chabwino tsopano chinasanduka imfa kwa ine? Si choncho ayi! Koma kuti uchimo uzindikirike kuti ndi uchimo unabala imfa mwa ine kudzera mu chomwe chinali chabwino, kotero kuti kudzera mu lamulo uchimo ukhale oyipa kopitirira. 14) Ife tikudziwa kuti Malamulo ndi auzimu; koma ine ndine munthu wofowoka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. 15) Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. 16) Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. 17) Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga. 18) Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita. 19) Ine sindichita zabwino zimene ndimafuna koma ndimachita zonyansa zimene sindikuzifuna. 20) Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga. 21) Tsono ndapeza kuti lamuloli likugwira ntchito. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, zoyipa zili nane pomwepo. 22) Mtima wanga umakondwera ndi lamulo la Mulungu. 23) Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga. 24) Kalanga ine! Adzandipulumutsa ndani ku thupi la imfali? 25) Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu! Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!