Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, James Chapter 1 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/James 1) Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana. Landirani moni. 2) Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. 3) Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. 4) Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. 5) Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. 6) Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. 7) Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. 8) Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita. 9) Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10) Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11) Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake. 12) Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda. 13) Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14) Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15) Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa. 16) Musanyengedwe abale anga okondedwa. 17) Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18) Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba. 19) Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20) Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21) Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani. 22) Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23) Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24) Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25) Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita. 26) Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27) Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi. Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!