< До римлян 16 >
1 Поручаю ж вам сестру́ нашу Фі́ву, служе́бницю Церкви в Кенхре́ях,
Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya.
2 щоб ви прийняли́ її в Господі, як личить святим, і допомагайте їй, у якій речі бу́де вона чого потребува́ти від вас, бо й вона опіку́нка була багатьом і самому мені.
Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.
3 Вітайте Приски́ллу й Аки́лу, співробітників моїх у Христі Ісусі, —
Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu.
4 що голови свої за душу мою клали, яким не я сам дякую, але й усі Церкви́ з поган, — і їхню домашню Це́ркву.
Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.
5 Вітайте улю́бленого мого Епене́та, — він пе́рвісток Азії для Христа.
Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo. Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.
6 Вітайте Марію, що напрацювалася багато для вас.
Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.
7 Вітайте Андро́ніка й Юнія, родичів моїх і співв'язнів моїх, що славні вони між апо́столами, що й у Христі були перше мене.
Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.
8 Вітайте Амплія, мого улю́бленого в Господі.
Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.
9 Вітайте Урба́на, співробітника нашого в Христі, і улюбленого мого Стахі́я.
Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.
10 Вітайте Апелле́са, ви́пробуваного в Христі. Вітайте Аристову́лових.
Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu. Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.
11 Вітайте мого ро́дича Іродіо́на. Вітайте Нарки́сових, що в Господі.
Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga. Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.
12 Вітайте Трифе́ну й Трифо́су, що працюють у Господі. Вітайте улю́блену Перси́ду, що багато попрацювала в Господі.
Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika. Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.
13 Вітайте ви́браного в Господі Ру́фа, і матір його та мою.
Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.
14 Вітайте Асинкри́та, Фле́гонта, Єрма, Патро́ва, Єрмі́я і братів, що з ними.
Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.
15 Вітайте Філоло́га та Юлію, Ніре́я й сестру́ його, і Олімпія́на, і всіх святих, що з ними.
Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.
16 Вітайте один о́дного святим поцілунком. Вітають вас усі Церкви́ Христові!
Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.
17 Благаю ж вас, браття, щоб ви остерігалися тих, хто чинить розді́лення й згі́ршення проти науки, якої ви навчилися, і уникайте їх,
Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo.
18 бо такі не служать Господеві нашому Ісусу Христу, але власному череву; вони добрими та гарними словами зво́дять серця простодушних.
Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.
19 Ваша ж слухня́ність дійшла до всіх. І я тішусь за вас, але хо́чу, щоб були ви мудрі в доброму, а про́сті в злому.
Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.
20 А Бог миру потопче незаба́ром сатану під ваші но́ги. Благода́ть Господа нашого Ісуса Христа нехай буде з вами! Амі́нь.
Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu. Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.
21 Вітає вас мій співробі́тник Тимофі́й, і Лукі́й, і Ясон, і Сосипа́тр, мої родичі.
Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.
22 Вітаю вас у Господі й я, Те́ртій, що цього листа написав.
Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.
23 Вітає вас Гай, гости́нний для ме́не й ці́лої Церкви. Вітає вас міськи́й доморя́дник Ера́ст і брат Кварт.
Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni. Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.
Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.
25 А Тому́, хто може поставити вас міцно згідно з моєю Єва́нгелією й проповіддю Ісуса Христа, за об'я́вленням таємни́ці, що від вічних часі́в була замо́вчана, (aiōnios )
Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, (aiōnios )
26 а тепер ви́явлена, і через пророцькі писа́ння, з нака́зу вічного Бога, на по́слух вірі по всіх наро́дах прові́щена, — (aiōnios )
koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, (aiōnios )
27 єдиному мудрому Богові, через Ісуса Христа, слава навіки! Амі́нь. (aiōn )
kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni. (aiōn )