< До римлян 1 >

1 Павло, раб Ісуса Христа, покликаний [бути] апостолом і обраний, щоб звіщати Добру Звістку Бога,
Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu
2 яку Він сповістив раніше через Своїх пророків у Святих Писаннях.
umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake.
3 Це [Звістка] про Його Сина, Який за тілом був нащадком Давида,
Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide.
4 а за Духом святості був визнаний Сином Божим у силі через воскресіння з мертвих, – про Ісуса Христа, Господа нашого.
Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu,
5 Через Нього ми отримали благодать і апостольство, щоб заради Його імені [привести] до послуху віри всі народи,
ife tinalandira chisomo chokhala atumwi oyitana anthu a mitundu yonse kuti amukhulupirire ndi kumumvera mwachikhulupiriro kuti dzina lake lilemekezedwe.
6 серед яких і ви, покликані Ісуса Христа.
Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu.
7 Усім, хто в Римі, улюбленим Божим, покликаним святим. Благодать вам і мир від Бога, нашого Отця, і від Господа Ісуса Христа.
Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima. Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
8 Насамперед я дякую моєму Богові через Ісуса Христа за всіх вас, бо про вашу віру говорять у всьому світі.
Poyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akukamba za chikhulupiriro chanu.
9 Бог, Якому я служу моїм духом, звіщаючи Добру Звістку Його Сина, є моїм свідком, що я завжди пам’ятаю про вас і
Mulungu amene ndimamutumikira ndi mtima wanga onse polalikira Uthenga Wabwino wa Mwana wake, ndi mboni yanga kuti ndimakupemphererani nthawi zonse.
10 постійно прошу у своїх молитвах, щоби з волі Божої мені вдалося нарешті прийти до вас.
Mʼmapemphero anga, nthawi zonse, ndimapemphera kuti ngati nʼkotheka mwachifuniro cha Mulungu, njira inditsekukire kuti ndibwere kwanuko.
11 Прагну побачити вас, щоб розділити з вами якийсь духовний дар для вашого зміцнення,
Ine ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso zina zauzimu kuti zikulimbikitseni
12 щоб ми підбадьорили одне одного своєю спільною вірою – вашою й моєю.
ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake.
13 Не хочу, брати, щоб ви не знали, як багато разів я планував прийти до вас, аби мати якийсь плід серед вас, як і серед інших народів, але досі мав перешкоди.
Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa kuti nthawi zambiri ndakhala ndikufuna zobwera kwanuko, koma mpaka pano pali zolepheretsa, ndi cholinga choti ndidzapezeko zipatso pakati panupo monga momwe ndakhala ndikuchitira pakati pa a mitundu ina.
14 Я боржник перед еллінами й варварами, перед мудрими й неосвіченими.
Ine ndi wokakamizidwa ndi udindo wotumikira Agriki pamodzi ndi omwe si Agriki, kwa anzeru ndi kwa opusa omwe.
15 Саме тому я прагну звіщати Добру Звістку і вам у Римі.
Pa chifukwa chimenechi, ine ndikufunitsitsa kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso amene muli ku Roma.
16 Я не соромлюся Доброї Звістки Христа, оскільки вона є силою Божою для спасіння кожного, хто вірить, – спочатку юдея, а потім і язичника.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.
17 Адже в ній відкривається праведність Божа з віри у віру, як написано: «А праведник житиме вірою».
Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
18 Бо гнів Божий відкривається з неба проти усякої безбожності та неправедності людей, які своєю неправедністю придушують істину.
Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa.
19 Бо те, що можна знати про Бога, очевидно для них, адже Бог відкрив їм.
Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo.
20 Від створення світу невидимі якості Бога – Його вічна сила й божественна природа – були чітко зрозумілі у творінні, так що [люди] не мають виправдання, (aïdios g126)
Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula. (aïdios g126)
21 оскільки вони, знаючи Бога, не прославили Його як Бога й не дякували Йому, але їхні думки стали марними, а їхні нерозумні серця охопила темрява.
Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima.
22 Називаючи себе мудрими, вони стали нерозумними
Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa.
23 й проміняли славу нетлінного Бога на образи, подібні до смертної людини, птахів, тварин і плазунів.
Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.
24 Тому Бог віддав їх у гріховні бажання їхніх нечистих сердець, щоб вони самі між собою осквернили свої тіла.
Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo.
25 Вони проміняли Божу істину на неправду та поклонялися й служили творінню, а не Творцеві, Який є навіки благословенний. Амінь. (aiōn g165)
Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni. (aiōn g165)
26 Через це Бог віддав їх ганебним бажанням. Їхні жінки проміняли природні стосунки на неприродні.
Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo.
27 Так само й чоловіки відмовилися від природних стосунків із жінками й розпалилися пристрастю один до одного. Чоловіки з чоловіками роблять безсоромні вчинки й отримують самі в собі належне покарання за свої збочення.
Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.
28 Оскільки вони не вважали за потрібне пізнати Бога, то Бог віддав їх [їхньому] розпусному розуму, щоб вони робили те, чого не годиться робити.
Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo.
29 Вони сповнені всякої неправди, зла, жадібності та розпусти, сповнені заздрощів, убивств, чвар, обману та злоби. Вони поширюють плітки та
Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche,
30 наклепи, ненавидять Бога, вони нахабні, зарозумілі та хвалькуваті, вигадують, як зробити зло, не шанують батьків.
osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo,
31 У них немає розуміння, вони не виконують обіцянок, не мають любові та милосердя.
alibe nzeru, chikhulupiriro, sakhudzidwa mu mtima ndipo ndi ankhanza.
32 Хоча вони знають праведний наказ Божий про те, що всі, хто робить такі речі, заслуговують на смерть, вони не тільки продовжують їх робити, але й схвалюють тих, хто [це] робить.
Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.

< До римлян 1 >