< Mezmurlar 31 >

1 Müzik şefi için - Davut'un mezmuru Ya RAB, sana sığınıyorum. Utandırma beni hiçbir zaman! Adaletinle kurtar beni!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo; musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi; mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
2 Kulak ver bana, Çabuk yetiş, kurtar beni; Bir kaya ol bana sığınmam için, Güçlü bir kale ol kurtulmam için!
Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.
3 Madem kayam ve kalem sensin, Öncülük et, yol göster bana Kendi adın uğruna.
Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa, chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
4 Bana kurdukları tuzaktan uzak tut beni, Çünkü sığınağım sensin.
Ndimasuleni mu msampha umene anditchera pakuti ndinu pothawirapo panga.
5 Ruhumu ellerine bırakıyorum, Ya RAB, sadık Tanrı, kurtar beni.
Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga; womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.
6 Değersiz putlara bel bağlayanlardan tiksinirim, RAB'be güvenirim ben.
Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe; ine ndimadalira Yehova.
7 Sadakatinden ötürü sevinip coşacağım, Çünkü düşkün halimi görüyor, Çektiğim sıkıntıları biliyorsun,
Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu popeza Inu munaona masautso anga ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
8 Beni düşman eline düşürmedin, Bastığım yerleri genişlettin.
Inu simunandipereke kwa mdani koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.
9 Acı bana, ya RAB, sıkıntıdayım, Üzüntü gözümü, canımı, içimi kemiriyor.
Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto; maso anga akulefuka ndi chisoni, mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Ömrüm acıyla, Yıllarım iniltiyle tükeniyor, Suçumdan ötürü gücüm zayıflıyor, Kemiklerim eriyor.
Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula; mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso, ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Düşmanlarım yüzünden rezil oldum, Özellikle komşularıma. Tanıdıklarıma dehşet salar oldum; Beni sokakta görenler benden kaçar oldu.
Chifukwa cha adani anga onse, ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga; ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga. Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Gönülden çıkmış bir ölü gibi unutuldum, Kırılmış bir çömleğe döndüm.
Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira; ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Birçoğunun fısıldaştığını duyuyorum, Her yer dehşet içinde, Bana karşı anlaştılar, Canımı almak için düzen kurdular.
Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri; zoopsa zandizungulira mbali zonse; iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane, kuti atenge moyo wanga.
14 Ama ben sana güveniyorum, ya RAB, “Tanrım sensin!” diyorum.
Koma ndikudalira Inu Yehova; ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Hayatım senin elinde, Kurtar beni düşmanlarımın pençesinden, Ardıma düşenlerden.
Masiku anga ali mʼmanja mwanu; ndipulumutseni kwa adani anga ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Yüzün kulunu aydınlatsın, Sevgi göster, kurtar beni!
Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu; pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
17 Utandırma beni, ya RAB, sana sesleniyorum; Kötüler utansın, ölüler diyarında sesleri kesilsin. (Sheol h7585)
Yehova musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndalirira kwa Inu; koma oyipa achititsidwe manyazi ndipo agone chete mʼmanda. (Sheol h7585)
18 Sussun o yalancı dudaklar; Doğru insana karşı Gururla, tepeden bakarak, Küçümseyerek konuşan dudaklar.
Milomo yawo yabodzayo ikhale chete, pakuti chifukwa cha kunyada ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.
19 İyiliğin ne büyüktür, ya RAB, Onu senden korkanlar için saklarsın, Herkesin gözü önünde, Sana sığınanlara iyi davranırsın.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwawasungira amene amakuopani, umene mumapereka anthu akuona kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
20 İnsanların düzenlerine karşı, Koruyucu huzurunla üzerlerine kanat gerersin; Saldırgan dillere karşı Onları çardağında gizlersin.
Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa, kuwateteza ku ziwembu za anthu; mʼmalo anu okhalamo mumawateteza kwa anthu owatsutsa.
21 RAB'be övgüler olsun, Kuşatılmış bir kentte Sevgisini bana harika biçimde gösterdi.
Matamando akhale kwa Yehova, pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
22 Telaş içinde demiştim ki, “Huzurundan atıldım!” Ama yardıma çağırınca seni, Yalvarışımı işittin.
Ndili mʼnkhawa zanga ndinati, “Ine ndachotsedwa pamaso panu!” Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.
23 RAB'bi sevin, ey O'nun sadık kulları! RAB kendisine bağlı olanları korur, Büyüklenenlerin ise tümüyle hakkından gelir.
Kondani Yehova oyera mtima ake onse! Yehova amasunga wokhulupirika koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
24 Ey RAB'be umut bağlayanlar, Güçlü ve yürekli olun!
Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima, inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

< Mezmurlar 31 >