< Süleyman'In Özdeyişleri 28 >
1 Kötü kişi kendisini kovalayan olmasa bile kaçar, Doğrularsa genç aslan gibi yüreklidir.
Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa, koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.
2 Ayaklanan ülke çok başlı olur, Ama akıllı, bilgili kişi düzeni sağlar.
Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri, koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.
3 Yoksulu ezen yoksul, Ürünü harap eden sağanak yağmur gibidir.
Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.
4 Yasayı terk eden kötüyü över, Yerine getirense kötüye karşı çıkar.
Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa, koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.
5 Kötüler adaletten anlamaz, RAB'be yönelenlerse her yönüyle anlar.
Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama, koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.
6 Dürüst bir yoksul olmak, Yolsuzlukla zengin olmaktan yeğdir.
Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.
7 Kutsal Yasa'yı yerine getiren çocuk akıllıdır, Oburlarla arkadaşlık edense babasını utandırır.
Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu, koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.
8 Faiz ve tefecilikle malına mal katan kişi, Bunu yoksullara acıyan için biriktirir.
Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.
9 Yasaya kulağını tıkayanın Duası da iğrençtir.
Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.
10 Dürüst kişileri kötü yola saptıran Kendi kazdığı çukura düşer. İyiliği, özü sözü bir olanlar miras alacak.
Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa adzagwera mu msampha wake womwe, koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.
11 Zengin kendini bilge sanır, Ama akıllı yoksul onun içini okur.
Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.
12 Doğruların zaferi coşkuyla kutlanır, Ama kötüler egemen olunca insan kaçacak yer arar.
Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu; koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.
13 Günahlarını gizleyen başarılı olmaz, İtiraf edip bırakansa merhamet bulur.
Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
14 Günahtan çekinen ne mutludur! İnatçılık edense belaya düşer.
Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse, koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.
15 Yoksul halkı yöneten kötü kişi Kükreyen aslan, saldırgan ayı gibidir.
Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.
16 Gaddar önderin aklı kıttır; Haksız kazançtan nefret edense uzun ömürlü olur.
Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.
17 Adam öldürmekten vicdan azabı çeken, mezara dek kaçacaktır; Kimse ona yardım etmesin.
Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.
18 Alnı ak yaşayan kurtulur, Yolsuzluk yapan ansızın yıkıma uğrar.
Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.
19 Toprağını işleyenin ekmeği bol olur, Hayal peşinde koşansa yoksulluğa doyar.
Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.
20 Güvenilir kişi bolluğa erer, Zengin olmaya can atansa beladan kurtulamaz.
Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
21 Hatır gözetmek iyi değildir, Çünkü insan bir lokma ekmek için bile suç işler.
Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
22 Cimri servet peşinde koşar, Yoksulluğa uğrayacağını düşünmez.
Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.
23 Başkasını azarlayan sonunda Pohpohlayandan daha çok beğeni kazanır.
Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.
24 Annesini ya da babasını soymayı günah saymayan, Haydutla birdir.
Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.
25 Açgözlü kavga çıkarır, RAB'be güvenense bolluk içinde yaşar.
Munthu wadyera amayambitsa mikangano, koma amene amadalira Yehova adzalemera.
26 Kendine güvenen akılsızdır, Bilgece davranan güvenlikte olur.
Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.
27 Yoksula verenin eksiği olmaz, Yoksulu görmezden gelense bir sürü lanete uğrar.
Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.
28 Kötüler egemen olunca insan kaçacak yer arar, Ama kötüler yok olunca doğrular çoğalır.
Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala, koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.