< Yeremya 38 >
1 Mattan oğlu Şefatya, Paşhur oğlu Gedalya, Şelemya oğlu Yehukal ve Malkiya oğlu Paşhur Yeremya'nın halka söylediği şu sözleri duydular:
Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti,
2 “RAB diyor ki, ‘Bu kentte kalan kılıçtan, kıtlıktan, salgından ölecek. Kildaniler'e gidense sağ kalacak, canını kurtarıp yaşayacak.’
“Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo.
3 RAB diyor ki, ‘Bu kent kesinlikle Babil Kralı'nın ordusuna teslim edilecek, Babil Kralı onu ele geçirecek.’”
Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’”
4 Önderler krala, “Bu adam öldürülmeli” dediler, “Çünkü söylediği bu sözlerle kentte kalan askerlerin ve halkın cesaretini kırıyor. Bu adam halkın yararını değil, zararını istiyor.”
Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”
5 Kral Sidkiya, “İşte o sizin elinizde” diye yanıtladı, “Kral size engel olamaz ki.”
Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.”
6 Böylece Yeremya'yı alıp kralın oğlu Malkiya'nın muhafız avlusundaki sarnıcına halatlarla sarkıtarak indirdiler. Sarnıçta su yoktu, yalnız çamur vardı. Yeremya çamura battı.
Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.
7 Sarayda görevli hadım Kûşlu Ebet-Melek Yeremya'nın sarnıca atıldığını duydu. Kral Benyamin Kapısı'nda otururken,
Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini.
8 Ebet-Melek saraydan çıkıp kralın yanına gitti ve ona şöyle dedi:
Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti,
9 “Efendim kral, bu adamların Peygamber Yeremya'ya yaptıkları kötüdür. Onu sarnıca attılar, orada açlıktan ölecek. Çünkü kentte ekmek kalmadı.”
“Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”
10 Bunun üzerine kral, “Buradan yanına üç adam al, Peygamber Yeremya'yı ölmeden sarnıçtan çıkarın” diye ona buyruk verdi.
Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”
11 Ebet-Melek yanına adamları alarak saray hazinesinin alt odasına gitti. Oradan eski bezler, yırtık pırtık giysiler alıp halatlarla sarnıca, Yeremya'ya sarkıttı.
Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya.
12 Sonra Yeremya'ya, “Bu eski bezleri, yırtık giysileri halatlarla bağlayıp koltuklarının altına geçir” diye seslendi. Yeremya söyleneni yaptı.
Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi,
13 Onu halatlarla çekip sarnıçtan çıkardılar. Yeremya muhafız avlusunda kaldı.
ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.
14 Kral Sidkiya Peygamber Yeremya'yı RAB'bin Tapınağı'nın üçüncü girişine getirterek, “Sana bir şey soracağım” dedi, “Benden bir şey gizleme.”
Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”
15 Yeremya, “Sana bir şey bildirirsem, beni öldürmeyecek misin?” diye karşılık verdi, “Üstelik öğüt versem bile beni dinlemeyeceksin.”
Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.”
16 Kral Sidkiya, “Bize yaşam veren RAB'bin varlığı hakkı için seni öldürmeyeceğim, canının peşinde olan bu adamların eline seni teslim etmeyeceğim” diyerek gizlice ant içti.
Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.”
17 Bunun üzerine Yeremya Sidkiya'ya şu karşılığı verdi: “İsrail'in Tanrısı, Her Şeye Egemen RAB Tanrı diyor ki, ‘Babil Kralı'nın komutanlarına teslim olursan, canın bağışlanacak, bu kent de ateşe verilmeyecek. Sen de ailen de sağ kalacaksınız.
Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo.
18 Ama Babil Kralı'nın komutanlarına teslim olmazsan, kent Kildaniler'e teslim edilecek, onu ateşe verecekler. Sen de onlardan kaçıp kurtulamayacaksın.’”
Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’”
19 Kral Sidkiya, “Kildaniler'in tarafına geçen Yahudiler'den korkuyorum” dedi, “Kildaniler beni onların eline verebilir, onlar da bana kötü davranırlar.”
Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”
20 “Vermezler” diye yanıtladı Yeremya, “Lütfen sana aktardığım RAB'bin sözünü işit. O zaman sağ kalır, iyilik görürsün.
Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa.
21 Ama teslim olmak istemezsen, RAB bana şunu açıkladı:
Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi:
22 Yahuda Kralı'nın sarayında kalan bütün kadınlar Babil Kralı'nın komutanlarına çıkarılacak. O kadınlar sana, “‘Güvendiğin insanlar Seni aldatıp yenilgiye uğrattı; Çamura battı ayakların, Güvendiğin insanlar seni bırakıp gitti’ diyecekler.
Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti, “‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa, ndipo anakugonjetsa. Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope; abwenzi ako aja akusiya.’
23 “Bütün karıların, çocukların Kildaniler'e teslim edilecek. Sen de onlardan kaçıp kurtulamayacak, Babil Kralı'nın eliyle yakalanacaksın. Bu kent ateşe verilecek.”
“Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.”
24 Sidkiya, “Ölmek istemiyorsan, konuştuklarımızı kimse duymasın” dedi,
Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa.
25 “Görevliler seninle konuştuğumu duyup da gelir, ‘Krala ne söyledin, kral sana ne dedi, açıkla bize, bizden gizleme! Yoksa seni öldürürüz’ derlerse,
Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’
26 ‘Beni Yonatan'ın evine geri gönderme, yoksa orada ölürüm diye krala yalvardım’ dersin.”
udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’”
27 Bütün görevliler gelip Yeremya'yı sorguya çektiler. Yeremya kralın kendisine söylemesini buyurduğu her şeyi onlara anlattı. Sorguyu bıraktılar. Çünkü kralla yaptığı konuşma duyulmamıştı.
Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.
28 Yeremya Yeruşalim'in ele geçirildiği güne dek muhafız avlusunda kaldı.
Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.