< Psaltaren 67 >

1 En Psalmvisa, till att föresjunga på strängaspel. Gud vare oss nådelig, och välsigne oss; han låte sitt ansigte lysa oss; (Sela)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire.
2 Att vi på jordene måge känna hans väg, ibland alla Hedningar hans salighet.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.
3 Gud, dig tacke folk; all folk tacke dig.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
4 Folken fröjde sig och glädjes, att du dömer folken rätt, och regerar folken på jordene. (Sela)
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
5 Gud, dig tacke folk; all folk tacke dig.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
6 Landet gifver sina frukt. Gud, vår Gud välsigna oss.
Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu.
7 Gud välsigne oss, och all verlden frukte honom.
Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

< Psaltaren 67 >